Num. 36 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choloŵa cha akazi okwatiwa

1Atsogoleri a banja la ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase, limodzi mwa mabanja a adzukulu a Yosefe, adabwera kudzalankhula ndi Mose ndi atsogoleri, akulu a mabanja a makolo a Aisraele.

2Num. 27.7 Iwowo adati, “Chauta adakulamulani inu mbuyathu kuti mutachita maere, mupatse Aisraele dziko, kuti likhale choloŵa chao. Ndiponso inu mbuyathu, Chauta adakulamulani kuti mupatse choloŵa cha mbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi.

3Koma ngati akwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisraele, choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha makolo athu ndi kuwonjezera pa choloŵa cha fuko la amuna aowo, motero choloŵa chathu chidzachepa.

4Ndipo chikafika chikondwerero cha Aisraele cha chaka cha 50, choloŵa chaocho chidzaonjezedwa pa choloŵa cha fuko la amuna ao. Motero choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha fuko la makolo athu.”

5Pamenepo Mose adaŵalamula Aisraele potsata mau a Chauta, adati, “Zimene akunena ana a Yosefezi nzoona.

6Zomwe Chauta akulamula za ana aakazi a Zelofehadi ndi izi: Aloleni akwatiwe ndi yemwe akumufuna, malinga akwatiwe ndi a m'banja la fuko la makolo ao.

7Choloŵa cha Aisraele chisachotsedwe m'fuko lina nkuchipatsa fuko lina. Pakuti Mwisraele aliyense ayenera kukangamira pa choloŵa cha fuko la makolo ake.

8Mkazi aliyense amene alandira choloŵa m'fuko lililonse la Aisraele, akwatiwe ndi ana a abale a bambo wao. Mwisraele aliyense adzalandira choloŵa cha makolo ake.

9Choncho palibe choloŵa chimene chidzachotsedwe m'fuko lina kupatsidwa ku fuko lina. Pajatu fuko lililonse la Aisraele lidzakangamira pa choloŵa chake.”

10Ana aakazi a Zelofehadi adachitadi zomwe Mulungu adalamula Mose.

11Mala, Tiriza, Hogola, Milika ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, adakwatiwa ndi ana a abale a bambo wao.

12Adakwatiwa ndi a m'mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, ndipo choloŵa chao chidakhalabe m'fuko la bambo wao.

13Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Aisraele kudzera mwa Mose. Adaperekedwa m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help