Hos. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Efuremu chakudya chake ndi mpweya wokhawokha.

Amanka nasaka mphepo yakuvuma tsiku lonse.

Amachulukitsa mabodza ndi chiwawa.

Amachita chipangano ndi dziko la Asiriya,

ndipo amapereka mitulo ya mafuta ku Ejipito.”

2Chauta akuŵaimba mlandu anthu a ku Yuda.

Adzalanga a m'banja la Yakobe

chifukwa cha makhalidwe ao,

adzaŵabwezera zolingana ndi ntchito zao zoipa.

3 Gen. 25.26 Gen. 32.24-26 Akali m'mimba mwa mai wake,

Yakobe adakangana ndi mbale wake,

ndipo atakula adalimbana ndi Mulungu.

4 Gen. 28.10-22 Yakobeyo adalimbana ndi mngelo ndipo adapambana.

Adalira napempha madalitso.

Mulungu adakumana naye ku Betele,

ndipo kumeneko podzera mwa iyeyo adalankhula nafe.

5Ameneyu ndiye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.

Anthu azimkumbukira ndi dzina lakeli loti Chauta.

6Motero bwererani nonsenu

ndi chithandizo cha Mulungu wanu.

Mukhale achikondi ndi olungama,

ndipo muzidalira Mulungu wanu nthaŵi zonse.

Alankhulabe za chilango

7Chauta akuti,

“Aisraele ali ngati wamalonda wonyenga

amene amagwiritsa ntchito masikelo onama.

Amakonda kumeta anthu.

8Aefuremu akunena kuti,

‘Ndithu talemera,

takhuphuka zedi,

wina sangatiloze chala pa kulemera kumeneku.’

9 Lev. 23.42, 43 Koma Ine ndine Chauta, Mulungu wanu,

amene ndidakutulutsani ku Ejipito.

Ndidzakukhalitsaninso m'mahema,

monga munkachitira masiku amakedzana m'chipululu muja.

10Ndidalankhula ndi aneneri.

Ndine amene ndidaŵaonetsa zinthu zambiri ngati kutulo.

Ndidalankhula m'mafanizo kudzera mwa iwo.

11Komabe anthu ankapembedza mafano ku Giliyadi.

Ndithu mafano ameneŵa adzaonongedwa.

Ankapereka nsembe za nkhunzi ku Giligala,

koma maguwa ansembewo

ndidzaŵasandutsa miyulu ya miyala m'munda.”

12 Gen. 29.1-20 (Yakobe adathaŵira ku dziko la Aramu.

Israeleyo adagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi.

Ankaŵeta nkhosa kuti akwatire mkaziyo).

13 Eks. 12.50, 51 Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito

kudzera mwa mneneri.

Ndipo mwa mneneriyo adaŵasungabe.

14Koma Aefuremuwo adaputa mkwiyo wake,

nchifukwa chake Chauta adzaŵalanga ndi imfa.

Adzaŵalanga chifukwa adamchititsa manyazi kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help