Yos. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kugwetsedwa kwa mzinda wa Yeriko.

1Mzinda wa Yeriko udaali utatsekedwa pa zipata zake zonse, kuti Aisraele asaloŵe. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotuluka kapena kuloŵa mumzindamo.

2Chauta adauza Yoswa kuti, “Mvetsa! Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake amphamvu, ndakupatsa iwe.

3Iwe pamodzi ndi ankhondo, muzizungulira mzinda umenewu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku.

4Ansembe asanu ndi aŵiri, aliyense lipenga la nyanga yankhosa lili kumanja, ndiwo azitsogolera Bokosi lachipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, iwe ndi ankhondowo, mudzazungulire mzinda umenewu kasanunkaŵiri, ansembe akuliza malipengawo.

5Tsono adzalize mosalekeza ndi mwamphamvu zedi. Ndipo anthu akadzangomva kuliza koteroko, adzafuule kolimba, motero makoma a mzindawo adzagwa. Apo ankhondo ako onse adzaloŵa mumzindamo.”

6Pomwepo Yoswa adaitana ansembe naŵauza kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano ndipo ansembe asanu ndi aŵiri mwa inu apite patsogolo pa Bokosilo atanyamula malipenga a nyanga zankhosa, koma ankhondo ndiwo akhale patsogolo.”

7Ndipo adauza anthu kuti, “Yambamponi. Yendani mozungulira mzindawo, ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi lachipangano.”

8Tsono, potsata mau a Yoswa aja, ansembe asanu ndi aŵiri aja adapita patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta, akuliza malipenga a nyanga zankhosa zija.

9Ndipo ankhondo ndiwo anali patsogolo pa ansembe. Ankhondo ena anali pambuyo, ankatsatira Bokosi lachipanganolo. M'menemo nkuti malipenga ali pakati kulira.

10Koma Yoswa adalamula anthu kuti asafuule kapena kuchita phokoso mpaka iye atalamula.

11Motero ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja, adazungulira mzindawo kamodzi. Atatero, iwo ndi ankhondo adabwerera ku zithando, nakagona.

12Yoswa adauka m'mamaŵa, ndipo ansembewo adanyamulanso Bokosi lachipangano la Chauta.

13Ansembe asanu ndi aŵiri onyamula malipenga a nyanga zankhosa aja, adatsogolako akulizanso malipengawo. Ankhondo anali patsogolo, ndipo gulu lina la ankhondo linali kutsata pambuyo pa Bokosilo. Pamenepo nkuti malipenga ali pakati kulira.

14Pa tsiku lachiŵiri adauzunguliranso mzindawo kamodzi, nabwerera ku zithando. Adachita zimenezi masiku asanu ndi limodzi.

15Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, adadzuka m'mbandakucha, ndipo adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri. Ndi pa tsiku limenelo lokha pomwe adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri.

16Kuzungulira kwakasanunkaŵiri kutatha, ansembe aja akuliza malipenga, Yoswa adauza anthu kuti, “Fuulani! Chauta wakupatsani mzindawu.

17Mzindawu pamodzi ndi zonse za m'menemu muwononge, kuti zikhale ngati nsembe zopereka kwa Chauta. Koma Rahabu yekha wadama uja ndi onse a m'nyumba mwake, muŵasunge poti ndiye adabisa azondi athu aja.

18Koma inu, musatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukangotengako kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, ndipo zithando za Aisraele zidzaonongedwa.

19Koma zonse zasiliva ndi zagolide, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi zachitsulo zikhale zopatulika za Chauta.”

20Ahe. 11.30 Pomwepo ansembe adalizanso malipenga aja. Anthu atamva, adafuula kwambiri, ndipo linga la mzindawo lidagwa. Ndipo ankhondo onse adabwera nakaloŵa mu mzindawo, naulanda.

21Tsono adaloŵa mu mzinda, malupanga ali m'manja, napha onse ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, ana ndi nkhalamba zomwe. Adaphanso zoŵeta zonse, monga ng'ombe, nkhosa ndi abulu.

22Yoswa adauza anthu aŵiri amene adakazonda aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadamayo, ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake abwere kuno, monga mudamlonjezera.”

23Iwo adapita, nakatenga Rahabu pamodzi ndi bambo wake, mai wake, abale ake, ndi onse a m'banja laolo. Adabwera nawo onse a m'banja laolo naŵaika kuseri kwa zithando za Aisraele.

24Atatero, mzinda wonsewo adauthira moto, pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, kupatula zagolide ndi zasiliva, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi za chitsulo, zimene adatenga nazisunga mosungira chuma cha Nyumba ya Chauta.

25Ahe. 11.31 Koma Yoswa adamsiya ali moyo Rahabu wadama uja, pamodzi ndi abale ake onse, poti ndiye adaabisa azondi aja amene Yoswayo adaaŵatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabu zilipo pakati pa Aisraele mpaka lero lino.

26 1Maf. 16.34 Pa nthaŵi imeneyo Yoswa adapereka chenjezo motemberera kuti,

“Aliyense amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu,

Chauta adzamtemberere.

Aliyense amene adzamange maziko ake,

mwana wake wachisamba adzafa.

Aliyense amene adzamange zipata zake,

mzime wake adzafa.”

27Motero Chauta anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake idawanda m'dziko lonselo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help