Mphu. 28 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Munthu wokonda kulipsira anzake,

nayenso adzamulipsira Ambuye amene amaŵerenga machimo ake.

2 Mt. 6.14; Mk. 11.25 Ukakhululukira mnzako amene wakuchimwira,

nawenso Ambuye ukaŵapempha adzakukhululukira machimo ako.

3Ngati munthu asungira chiwembu mnzake,

angayembekeze bwanji kuti Ambuye adzamumvera chisoni?

4Ngati sachitira chifundo munthu mnzake,

angapemphe bwanji Ambuye kuti amkhululukire machimo ake?

5Ngati amene ali munthu chabe asunga mkwiyo,

osafuna kukhululukira mnzake,

iyeyo ndani adzamkhululukira zolakwa zake?

6Kumbukira kutha kwa moyo wako,

ndipo lekeratu chidani.

Kumbukira kuti udzafa ndi kuwola,

ndipo sunga Malamulo mokhulupirika.

7Ganiza za Malamulo ndipo usakwiyire mnzako.

Kumbukira chipangano cha Wopambanazonse,

ndipo ukhululukire mnzako.

Za kukangana

8Lewa kukangana ndi anzako,

ndipo udzachepetsa machimo ako,

chifukwa munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano.

9Munthu wochimwa amadzetsa mavuto pakati

pa abwenzi,

ndipo amautsa kusamvana pakati pa anthu

amene kale anali ndi mtendere.

10Moto umakolera chifukwa chosonkhezera,

ndeunso imakula ndi ukali wake.

Ukali wa munthu umalingana ndi mphamvu zake,

ndipo mkwiyo wake umakwera motsatana ndi chuma chake.

11Kukangana kwadzidzidzi kumautsa ndeu.

Ndipo ndeu yadzidzidzi imaphetsa.

12Mukauzira pa mbaliŵali, moto umayaka,

mukathirapo malovu, moto umazima.

Zonsezi zimachokera m'kamwa mwako.

Za kulankhula

13 Mphu. 51.2-6; Yak. 3.5-12 Akazitape ndi amthirakuŵiri afunika kuŵatemberera,

chifukwa adaononga anthu ambiri okhala mwamtendere.

14Akazitape adaononga anthu ambiri,

ndipo adaŵamwazira m'maiko ena ndi ena.

Adaononga mizinda yambiri yamalinga,

nagwetsa nyumba za anthu otchuka.

15Akazitape adasudzulitsa akazi okhulupirika

ndi kuŵalanda phindu lonse la ntchito zao.

16Aliyense amene amalabadako za ukazitape sadzapezanso pousa,

ndipo sadzakhala ndi mtendere mumtima mwake.

17Mkwapulo wa chikoti umasiya mikwingwirima,

koma mkwapulo wa lilime umaphwanya mafupa.

18Anthu ambiri adafa ndi lupanga,

koma amene adafa ndi lilime ngochuluka koposa.

19Ngwodala munthu amene amalewa

lilime lolongolola,

amene sadaone ukali wake,

amene sadasenze goli lake

ndipo sadamangidwe ndi unyolo wake.

20Paja goli lake nlachitsulo

ndipo matangadza ake ngamkuŵa.

21Lilimelo limadzetsa imfa yoŵaŵa,

ndipo nkwabwino kufa kupambana kukanthidwa

ndi lilime lotere.

22Koma silingathe kugonjetsa anthu oopa Mulungu,

iwo sangathe kupsa ndi moto wake.

23Anthu osiya Ambuye ndi amene adzazunzike nalo lilimelo,

lidzayaka ngati moto wosazima pakati pao.

Lidzaŵagwira ngati mkango

ndi kuŵang'amba pafupipafupi ngati kambuku.

24Monga munda wako umaumangira mpanda waminga,

monganso umatsekera siliva ndi golide wako,

25momwemonso uzichenjera ndi mau ako,

ndi kuŵapima bwino,

ndipo uziikapo chitseko ndi mipiringidzo pakamwa pako.

26Chenjera kuti lilime lako lingakulakwitse,

ungadzagwe m'manja mwa anthu okulalira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help