1 Mt. 4.15 Koma anthu amene anali ndi nkhaŵa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina.
Aneneratu za mfumu yam'tsogolo2 Mt. 4.16; Lk. 1.79 Anthu amene ankayenda mumdima
aona kuŵala kwakukulu.
Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani,
kuŵala kwaŵaonekera.
3Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu,
mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu.
Iwo akukondwa pamaso panu
monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika,
monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
4Pakuti inu mwathyola goli limene linkaŵalemera,
ndodo zimene ankamenyera mapewa ao,
ndiponso mikwapulo ya anthu oŵazunza,
monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani.
5Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo
ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi,
zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.
6Chifukwa mwana watibadwira,
mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife.
Ulamuliro udzakhala m'manja mwake,
ndipo adzamtchula dzina lake lakuti
“Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
7 Lk. 1.32, 33 Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira.
Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide,
ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake,
pochita zachilungamo ndi zangwiro
kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya.
Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse
watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Achenjeza Aisraele kuti adzalangidwa8Ambuye atumiza mau otsutsa Yakobe,
mauwo agwa pa Aisraele, zidzukulu zake.
9Anthu onse, ndiye kuti Aefuremu
ndi anthu okhala m'Samariya,
adzazimva zotsatira zake za mau ameneŵa.
Iwo amalankhula monyada ndi modzikuza kuti,
10“Ngakhale njerwa zagumuka,
ife tidzamanga ndi miyala yosema.
Ngakhale mitanda yamkuyu yagwetsedwa,
ife tidzaika mitanda yamkungudza m'malo mwake.”
11Koma Chauta waŵautsira adani,
Waŵakhwirizira adaniwo kuti amenyane nawo.
12Asiriya chakuvuma ndi Afilisti
chakuzambwe ayasama kukamwa kuti adye Aisraele.
Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke
chifukwa cha zonsezi,
ndipo mkono wake uli chisamulirecho
kufuna kuŵalanga.
13Anthuwo sadabwerere kwa Mulungu
amene adaŵakantha uja,
sadalape ndi kufunafuna Chauta Wamphamvuzonse.
14Nchifukwa chake Chauta wadula
mutu wa Israele pamodzi ndi mchira womwe,
nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe
pa tsiku limodzi.
15Mutuwo ukutanthauza akuluakulu ndi olemekezeka,
mchirawo ukutanthauza aneneri
ophunzitsa zabodza.
16Pakuti amene amatsogolera anthuŵa amaŵasokeza,
ndipo otsogoleredwawo amatayika.
17Nchifukwa chake Ambuye sadzakondwera nawo achinyamata,
ndipo sadzaŵachitira chifundo
ana amasiye ndi akazi amasiye.
Pakuti aliyense ndi wosasamala za Mulungu
ndiponso ndi wochimwa.
Pakamwa paliponse pamalankhula zopusa.
Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke
chifukwa cha zonsezi,
ndipo mkono wake uli chisamulirecho
kufuna kuŵalanga.
18Kuipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto,
moto wake wotentha mkandankhuku ndi minga.
Umayatsanso nkhalango
ndipo utsi wake umachita kuti toloo
ngati mtambo wochindikira.
19Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta
Wamphamvuzonse watentha dziko,
ndipo anthu ali ngati nkhuni zosonkhera moto.
Palibe munthu wochitira chifundo mbale wake.
20Ku dzanja lamanja amapeza ndi kudya
chakudya, koma osakhuta,
ku dzanja lamanzere amapeza ndi kudya
chakudya, koma njala ali nayobe.
Kwatsala nkumangodyana okhaokha.
21Amanase akuthira Aefuremu nkhondo,
Aefuremu akuthira Amanase nkhondo.
Onsewo pamodzi akumenyana ndi Yuda.
Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke
chifukwa cha zonsezi,
ndipo mkono wake uli chisamulirecho
kufuna kuŵalanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.