1Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala,
dziko louma lidzakondwa ndi kuchita maluŵa.
2Dzikolo lidzakhala ndi maluŵa ochuluka
ongodzimerera okha.
Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe.
Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe ake adzakhala okongola
ngati a ku Karimele ndi Saroni.
Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta
ndi ukulu wa Mulungu wathu.
3 Ahe. 12.12 Mulimbitse manja ofooka,
ndi kuŵapatsa mphamvu maondo olobodoka.
4Muuze onse a mtima wamantha kuti,
“Limbani mtima, musachite mantha.
Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu.
Akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Mt. 11.5; Lk. 7.22 Pamenepo maso a anthu akhungu adzaphenyuka,
ndipo makutu a agonthi adzatsekuka.
6Opunduka adzalumpha ngati mphoyo,
ndipo osalankhula adzaimba mokondwa.
Akasupe adzatumphuka m'chipululu,
ndipo mitsinje idzayenda m'dziko louma.
7Mchenga wotentha udzasanduka nyanja,
ndipo dziko louma lidzasanduka la akasupe.
Pamene panali mbuto za nkhandwe
padzamera udzu ndi bango.
8Kumeneko kudzakhala mseu waukulu
wotchedwa “Mseu Wopatulika.”
Ochimwa sadzayendamo,
ndipo zitsilu sizidzasokera m'menemo.
9Kumeneko sikudzakhala mikango,
ndipo nyama zoopsa sizidzafikako,
sizidzapezeka konse kumeneko.
Koma okhawo amene Chauta
adaŵapulumutsa,
adzayenda mu mseu umenewu.
10Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera,
ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala.
Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya,
ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo.
Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.