1Lisiyasi atapangana ndi Yudasi, adabwerera kwa mfumu, ndipo Ayuda adayamba kulima minda yao.
2Koma azibwanamkubwa ena a m'madera angapo, monga Timoteo ndi Apoloniyo mwana wa Geneo, ndiponso Yeronimo, Demofoni, ndiponso Nikanore, bwanamkubwa wa ku Kipro, sadaŵalole Ayuda kukhala mwamtendere.
3Anthu ena a ku Yopa adachita zamphulupulu monga izi: adaitana Ayuda amene ankakhala pakati pao, kuti abwere ndi akazi ao, ndi ana ao m'zombo zimene adaŵakonzera, kukhala ngati panalibe chidani konse pakati pao.
4Izi zinali zopangana anthu onse amumzindamo. Tsono Ayuda adavomera, ngati anthu ofuna mtendere, osaganiza kanthu koipa kalikonse. Koma atafika pakati pa nyanja, adaŵamiza m'madzi. Anthuwo anali ngati 200.
5Yudasi atamva zankhalwe zimene adaŵachita anthu a mtundu wake, adadziŵitsa ankhondo ake.
6Ndipo atapemphera kwa Mulungu, muweruzi wolungama, adapita kukaŵathira nkhondo anthu amene adaapha abale akewo. Adatentha nyumba za ku dooko ndi zombo zomwe nthaŵi yausiku, ndipo onse amene adathaŵiramo adaŵapha ndi lupanga.
7Popeza kuti zipata za mzindawo zinali zotseka, adachoka akuganiza zobwerera komweko msanga, kuti akaononge mzinda wonse wa Yopa.
8Koma Yudasi adamva kuti a ku Yaminiyanso ankaganiza zoŵachita zoterozo Ayuda akwao.
9Choncho adamenyana nawo nkhondo anthu a ku Yaminiyawo nthaŵi yausiku. Adatentha nyumba za ku dooko ndi zombo zomwe, kotero kuti malaŵi a moto ankaoneka mpaka ku Yerusalemu pa mtunda wa makilomita makumi asanu.
Yudasi apambana pa nkhondo ku chigawo cha Giliyadi10M'mene ankachoka ku Yaminiyako, atayenda mtunda wa pafupi makilomita aŵiri ncholinga cha kukachita nkhondo ndi Timoteo, kudafika Aluya 5,000 oyenda pansi ndi 500 okwera pa akavalo, kudzamenyana nawo nkhondo.
11Nkhondo idakula kwambiri, koma Mulungu ankaŵathandiza, motero Yudasi ndi anzake adagonjetsa adaniwo. Atagonjetsedwa, anthu osakhazikikawo adapempha Yudasi kuti akhale nawo pa ubwenzi, nalonjeza kuti adzapatsa Ayudawo ziŵeto ndi kumaŵathandiza pa zonse.
12Poganiza kuti iwowo angathedi kuŵathandiza pa zambiri, Yudasi adavomera kuti akhale pa mtendere; tsono iwowo atayanjana ndi Yudasi, adabwerera ku mahema ao.
13Pambuyo pake Yudasi adafuna kulanda mzinda wina umene eni ake adaulimbitsa ndi malinga adothi ndi makoma amiyala. M'menemo munali anthu akunja a mitundu yambiri. Mzindawo dzina lake linali Kaspini.
14Anthu amumzindamo ankakhulupirira mphamvu za malinga ao ndi kuchuluka kwa zakudya zao. Ankatukwana Ayuda nkumanena zachipongwe ndi kutchula zonyansa zolalatira Mulungu.
15Koma Yudasi ndi anthu ake, atapemphera Mwini dziko lapansi, amene adagumula malinga a Yeriko pa nthaŵi ya Yoswa, popanda zida zankhondo, adathamangira ku malinga mwaliŵiro ndi mwaukali.
16Adaulanda mzindawo malinga nkuti chinali chifuniro cha Mulungu. Adapha anthu ambirimbiri, kotero kuti nyanja imene inali pafupi pomwepo, yokwanira mamita 400 m'mimba mwake, inkaoneka ngati ikusefukira ndi magazi.
Yudasi agonjetsa ankhondo a Timoteo17Atachoka ku mzinda wa Kaspini, Yudasi ndi anthu ake adayenda ulendo wa makilomita 150 nkukafika ku Karaksi, kwa Ayuda otchedwa Atubi.
18Sadampeze Timoteo kumeneko. Iyeyo anali atachoka asanachite kanthu, koma adaasiya gulu lalikulu lankhondo pamenepo.
19Makaputeni aŵiri a Makabeo, Dosite ndi Sosipatere, adapita nakaononga anthu amene Timoteo adaaŵasiya kubomako. Onsewo pamodzi anali opitirira zikwi khumi.
20Tsono Makabeo adagaŵa khamu lake m'magulumagulu, naika anthu olamulira maguluwo. Atatero adathamanga kukakumana ndi Timoteo amene anali ndi ankhondo oyenda pansi 120,000 ndi okwera pa akavalo 2,500.
21Atamva kuti Yudasi akubwera, Timoteo adatumiza azimai, ana ndi katundu yemwe ku Karinaimu, chifukwa malo amenewo anali osatheka kuŵazinga ndi ovuta kufikako, poti njira zake zinali zophaphatiza pakati pa mapiri.
22Koma gulu loyamba la Yudasi litatulukira, adani ake adachita mantha nkuda nkhaŵa poona mphamvu za Mulungu woona zonse. Motero adayambapo kuthaŵa mwachipwirikiti, kotero kuti ambiri ankavulazana okhaokha pobayana ndi malupanga ao omwe.
23Tsono Yudasi adaŵalondola ndi mphamvu zonse, naŵabaya anthu ochimwawo; motero adapha anthu ngati 30,000 onse pamodzi.
24Timoteo yemwe adagwidwa ndi ankhondo a Dosite ndi a Sosipatere. Koma mochenjera adaŵapemba kuti amulole kungopita. Adaaŵabwatika ponena kuti iyeyo ankasunga abambo ao ndi abale ao ambiri m'ndende mwake, tsono iyeyo kufa, ndiye nawonso mbokafa.
25Adaŵakopa polankhula nawo mau ambiri nalonjeza kuti adzabweza anthuwo kwao osaŵavuta konse. Apo Ayuda aja adammasula Timoteo kuti apulumutse abale ao.
Yudasi apambananso26Pambuyo pake Yudasi adapita ku Karinaimu ndiponso ku nyumba yachipembedzo ya fano lotchedwa Atargatisi; kumeneko adapha anthu okwanira 25,000.
27Ataŵamwaza ndi kuŵaononga adaniwo, Yudasi uja adapita ndi ankhondo ake ku mzinda wamphamvu wa Efuroni, kumene Lisiyasi ankakhala ndi anthu ambirimbiri amitundumitundu. Achinyamata anyonga adakhala patsogolo pa malinga nkumamenya nkhondo molimbika kwambiri, ndipo m'kati mwa mzindawo munali zida zankhondo zambiri.
28Koma Ayuda adapemphera Mulungu Wamphamvuzonse amene mphamvu zake zimathyola kulimba kwa adani onse. Choncho adalanda mzindawo, napha anthu 25,000 amene ankakhala m'menemo.
29Atachoka kumeneko adathamangira ku Sitopoli, mzinda umene uli pa mtunda wa makilomita 120 kuchokera ku Yerusalemu.
30Koma Ayuda okhala kumeneko adauza Yudasi kuti anthu a ku Sitopoli ankaŵachitira zachifundo ndi kuyanjana nawo pa nthaŵi ya mavuto ao aakulu.
31Motero Yudasi ndi anzake adaŵathokoza anthu a ku Sitopoli, naŵauza kuti asaleke kumaŵachitira zachifundo anthu a mtundu wao. Pambuyo pake adafika ku Yerusalemu nthaŵi ili pafupi yoyambira chikondwerero cha Masabata.
Yudasi agonjetsa Gorjiyasi32 atamenya nkhondo nthaŵi yaitali, adayamba kufooka ndi kutopa. Pamenepo Yudasi adapemphera kwa Ambuye kuti aŵathandize ndi kukhala mtsogoleri wao pa nkhondoyo.
37Tsono Yudasi atayamba kuimba nyimbo m'chilankhulo cha makolo ake, ngati nyimbo yankhondo, Ayuda adalumphira anthu a Gorjiyasi moŵadzidzimutsa nkuŵapirikitsa.
Mapemphero opempherera anthu ofera ku nkhondo38Pambuyo pake Yudasi adasonkhanitsa ankhondo ake napita ku mzinda wa Adulamu, koma poti linkafika tsiku lachisanu ndi chiŵiri, adadziyeretsa monga momwe adaazoloŵerera, ndipo adalemekeza tsiku la Sabatalo komweko.
39M'maŵa mwake kunali kofunika kwambiri kuti azinyamula mitembo ya anzao amene adaphedwa aja, kukaŵaika ndi abale ao m'manda a makolo ao.
40Deut. 7.25Koma aliyense mwa ophedwawo m'kati mwa mkanjo wake adampeza atavala zinthu zina zoperekedwa ku mafano a ku Yaminiya, zinthu zoletsedwa ndi Malamulo a Ayuda. Pamenepo onse adazindikira kuti anthuwo adafa chifukwa cha chimenecho.
41Onse adayamika njira za Ambuye, Muweruzi wolungama, amene amaonetsa poyera zinthu zobisika.
42Ndipo adayamba kupemphera, kupempha Ambuye kuti afafaniziretu tchimo laolo. Motero Yudasi, munthu uja, adalangiza anthu ake kuti apewe machimo, popeza kuti anali atadziwonera okha zimene zidaagwera anzaowo chifukwa cha tchimo lao.
43Tsono adachita msonkhamsonkha mwa anthu ake onse nkupeza ndalama 2,000 zasiliva, nazitumiza ku Yerusalemu, kuti akaperekere nsembe zopepesera machimo. Pakutero, adachita chinthu chokoma ndi chachikulu kwambiri, chifukwa chokhulupirira za kuuka kwa akufa.
44Chikadakhala chinthu chopusa ndi chopanda ntchito kupempherera akufa, achikhala kuti sankakhulupirira kuti akufawo adzaukadi.
45Maganizo otere a Yudasi anali aakulu ndi okoma. Ankakhulupirira kuti anthu onse otumikira Mulungu adzalandira mphotho yokoma. Nchifukwa chake adapereka nsembe yopepesera machimo, kuti akufa aja amasulidwe m'zoipa zao.
Menelasi aphedwaWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.