1Chauta akuti,
“Lizani lipenga!
Adani akugudukira dziko la Chauta
ngati adembo pamwamba pa nyama.
Anthu anga aphwanya chipangano changa,
ndipo achimwira malamulo anga.
2Amalirira kwa Ine kuti ndiŵathandize,
amati,
‘Ife Aisraele tikukudziŵani Inu Mulungu wathu.’
3Koma Aisraele akana zabwino.
Nchifukwa chake adani ao adzaŵapirikitsa.
4“Amadzilongera mafumu mosatsata kufuna kwanga.
Amadziikira atsogoleri popanda chilolezo changa.
Adzipangira mafano asiliva ndi agolide,
koma adziwononga nawo.
5Fano la mwanawang'ombe
limene a ku Samariya akupembedza likundinyansa.
Motero mkwiyo wanga waŵayakira kwambiri anthuwo.
Padzapita nthaŵi yaitali chotani asanasinthe
kuti ayere anthu a ku Israele?
6“Fanolo si mulungu konse,
adalipanga ndi munthu waluso.
Fano la ku Samariyali lidzatswanyidwa pafupipafupi.
7“Aisraele amafesa kamphepo,
ndipo amakolola kamvulumvulu.
Tirigu alibe ngala,
sadzabala chakudya.
Akadabala,
alendo akadadya chakudyacho.
8Aisraele amezedwa.
Asanduka ngati chiŵiya chachabe
pakati pa anthu a mitundu ina.
9Adathaŵira ku Asiriya
ngati mbidzi yongodziyendera payokha.
Aefuremu adalipira anthu a ku maiko ena
kuti akhale oŵathandiza.
10Chifukwa choti adagwirizana ndi anthu a mitundu ina,
ndidzaŵasonkhanitsa ndi kuŵaononga.
Posachedwa adzazunzika kwambiri
chifukwa cha ulamuliro wa mfumu ya ku Asiriya.
11“Aefuremu adachulukitsa maguwa ansembe
ochotserapo machimo,
koma maguwawo asanduka malo ochimwirapo.
12Ndidaŵapatsa malamulo ambiri olembedwa,
koma saŵasamala.
Amaŵayesa achilendo.
13Amapereka nsembe zanyama kwa Ine nkumadya,
koma Ine Chauta sindikondwera nazo konse.
Sindidzaiŵala zolakwa zao,
ndidzaŵalanga chifukwa cha zimenezo.
Ndidzaŵabwezera ku ukapolo ku Ejipito.
14Aisraele adzimangira nyumba zikuluzikulu,
kuiŵala Mlengi wao.
Ayuda achulukitsa mizinda yamalinga.
Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yaoyo,
ndipo motowo udzatentha nyumba zao zazikuluzo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.