1 Num. 26.1-51 Chauta adalankhula ndi Mose ku chipululu cha Sinai, m'chihema chamsonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, chaka chachiŵiri atatuluka ku dziko la Ejipito, ndipo adamuuza kuti,
2“Uŵerenge anthu a mpingo wonse wa Aisraele potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ulembe dzina la munthu wamwamuna aliyense mmodzimmodzi.
3Iwe ndi Aroni muŵerenge anthu, gulu ndi gulu, a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, ndiye kuti anthu onse a ku Israele amene angathe kumenya nkhondo.
4Pa fuko lililonse mutenge munthu mmodzi, mtsogoleri wa banja lake, kuti akuthandizeni pa ntchito yanuyo.
5Maina a anthu okuthandizaniwo ndi aŵa: fuko la Rubeni, akuthandizeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri;
6fuko la Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai;
7fuko la Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu;
8fuko la Isakara, Netanele mwana wa Zuwara;
9fuko la Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.
10Mwa ana a Yosefe: fuko la Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; fuko la Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri;
11fuko la Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni;
12fuko la Dani, Ahiyezere mwana wa Amishadai;
13fuko la Asere, Pagiyele mwana wa Okarani;
14fuko la Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele;
15fuko la Nafutali, Ahira mwana wa Enani.”
16Ameneŵa ndiwo anthu amene adasankhidwa mu mpingo, atsogoleri a mabanja ao, akulu a mafuko a Aisraele.
17Mose ndi Aroni adaŵatenga anthu amene atchulidwaŵa,
18ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, adasonkhanitsa mpingo wonse. Tsono Aisraele adalembetsa maina ao potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ankalembetsa ndi anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo, mmodzimmodzi,
19monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Umu ndi m'mene adaŵerengera anthuwo m'chipululu cha Sinai.
20Mwa zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wa Yakobe, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
21Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Rubeni, adapezeka kuti ali 46,500.
22Mwa zidzukulu za Simeoni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
23Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Simeoni, adapezeka kuti ali 59,300.
24Mwa zidzukulu za Gadi adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
25Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Gadi, adapezeka kuti ali 45,650.
26Mwa zidzukulu za Yuda adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
27Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Yuda, adapezeka kuti ali 74,600.
28Mwa zidzukulu za Isakara adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
29Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Isakara, adapezeka kuti ali 54,400.
30Mwa zidzukulu za Zebuloni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
31Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Zebuloni, adapezeka kuti ali 57,400.
32Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
33Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Efuremu, adapezeka kuti ali 40,500.
34Mwa zidzukulu za Manase adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
35Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Manase, adapezeka kuti ali 32,200.
36Mwa zidzukulu za Benjamini adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
37Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Benjamini, adapezeka kuti ali 35,400.
38Mwa zidzukulu za Dani adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
39Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Dani, adapezeka kuti ali 62,700.
40Mwa zidzukulu za Asere adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
41Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Asere, adapezeka kuti ali 41,500.
42Mwa zidzukulu za Nafutali adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
43Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Nafutali, adapezeka kuti ali 53,400.
44Ameneŵa ndiwo anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, mothandizidwa ndi atsogoleri a Aisraele khumi ndi aŵiri amene ankaimirira mafuko ao.
45Choncho amuna onse a mu Israele otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata banja la makolo ao,
46adapezeka kuti ali 603,550.
47Alevi okha sadaŵaŵerengere kumodzi ndi enawo, potsata banja la makolo ao,
48chifukwa Chauta adaauza Mose kuti,
49“Fuko la Levi usaliŵerenge ai, anthu ake usaŵalembere kumodzi ndi Aisraele enawo.
50Uike Aleviwo kuti aziyang'anira chihema changa chaumboni, zipangizo zake ndi zonse zimene zili m'menemo. Azinyamula chihemacho, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo azichisamala. Zithando zao azimange pozungulira chihemacho.
51Nthaŵi imene anthu akunyamuka ulendo, Alevi ndiwo amene azichitsitsa, ndipo nthaŵi imene anthu aima, Alevi omwewo ndiwo amene azichiimiritsa. Munthu wina aliyense wochiyandikira adzaphedwa.
52Aisraele azimanga mahema ao m'magulumagulu, aliyense pa chithando chake, ndipo onse azimanga pafupi ndi mbendera yao.
53Koma Alevi amange mahema ao pozungulira chihema chaumboni, kuti Mulungu asakwiyire mpingo wa Aisraele. Alevi ndiwo amene aziyang'anira chihema chaumbonicho.”
54Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.