Ezek. 35 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu adzalanga Edomu

1 ndipo ulengeze mau oliimba mlandu.

3Anthu akumeneko uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi:

“Inu anthu a ku mapiri a ku Seiri ndikudana nanu.

Ndidzakumenyani ndi dzanja langa,

ndidzasandutsa dziko lanu tsala ndi chipululu.

4Mizinda yanu ndidzaisandutsa mabwinja,

ndipo dziko lanu lidzakhala chipululu.

Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

5“Munali adani a Israele nthaŵi zonse, ndipo munkalola kuti anthu ake aziphedwa pa nthaŵi ya mavuto ao, pa nthaŵi imene chilango chao chidafika pa chimake.

6Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Pali Ine ndemwe, ndidzakhetsa magazi anu, ndipo imfa idzakulondolani. Zoonadi, mudakhetsa magazi, tsono imfa idzakulondolani.

7Phiri la Seiri ndidzalisandutsa tsala ndi chipululu. Ndidzapha onse amene amayenda kumeneko.

8Mapiri ake ndi zigwa zake ndidzazidzaza ndi mitembo, tsono ophedwa pa nkhondo adzangoti vuu pa magomo, m'zigwa ndi m'mitsinje yanu.

9Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya, ndipo m'mizinda mwanu simudzakhalanso munthu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’

10“Inu mudanena kuti, ‘Mitundu iŵiri ya anthu, Yuda ndi Israele, idzakhala yathu pamodzi ndi maiko ao omwe.’ Mudatero ngakhale kuti Ine Chauta ndinali nao m'menemo.

11Tsono Ine Ambuye Mulungu ndikuti, Pali Ine ndemwe, ndidzakuchitani zomwe mudaŵachita anthu anga poŵaonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu. Mudzandidziŵadi pakati panupo, ndikadzakulangani.

12Mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndidamva mau anu onse onyoza mapiri a ku Israele. Mudanena kuti, ‘Mapiri a ku Israele asiyidwa, ndipo atipatsa kuti tiŵaononge.’

13Ndidamva zondinyoza zimene mudanena monyada. Ndidadzimvera ndekha zonse!

14Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakusandutsani bwinja kotheratu, kotero kuti dziko lonse lapansi lidzakondwa nako kugwa kwanu.

15Monga momwe inu mudakondwera ndi kugwa kwa Israele, Ine ndidzakuchitaninso zomwezo. Iwe phiri la Seiri, ndi dziko lonse la Edomu, udzasanduka bwinja. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help