Mas. 141 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lamadzuloSalmo la Davide.

1Ndikukuitanani, Inu Chauta,

fulumirani kudzandithandiza.

Tcherani khutu kuti mumve liwu langa

pamene ndikupemphera kwa Inu.

2 Chiv. 5.8 Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani,

kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

3Muike mlonda pakamwa panga, Inu Chauta.

Mulonde pa khomo la milomo yanga.

4Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa,

ndisadzipereke ku ntchito zoipa

pamodzi ndi anthu ochita zoipa,

ndisadye nawo maphwando ao.

5Munthu wolungama angathe kundimenya

kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo,

koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa,

pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.

6Anthu oipa akadzaperekedwa kwa oŵalanga,

pamenepo adzaphunzira kuti mau a Chauta ndi oona.

7Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziŵaza,

ndi m'menenso mafupa ao adzamwazikira ku manda.

8Koma maso anga amayang'anirabe kwa Inu,

Chauta Mulungu wanga.

Ndimathaŵira kwa Inu kuti munditeteze,

musandisiye opanda wonditchinjiriza.

9Mundipulumutse ku msampha umene iwo anditchera,

ndi ku makhwekhwe a anthu ochita zoipa.

10Anthu oipa akodwe pamodzi mu ukonde wao womwe,

koma ine ndipulumuke.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help