1Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yehu, mwana wa Hanani, mau odzudzula Baasa akuti,
2“Iwe sudaali kanthu konse, ndidachita kukukweza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele. Komabe tsopano wachimwa ngati Yerobowamu, ndipo waŵachimwitsa anthu a ku Israelewo, mwakuti iwo aputa mkwiyo wanga chifukwa cha kuchimwa kwaoko.
3Ndithudi ndidzakufafaniza kotheratu pamodzi ndi banja lako lonse, monga m'mene ndidachitira banja la Yerobowamu mwana wa Nebati.
4Aliyense wa banja la Baasa amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zamumlengalenga zidzamudya.”
5Ntchito zina za Baasa ndi zonse zamphamvu zimene adachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
6Baasa adamwalira, naikidwa m'manda ku Tiriza. Ndipo Ela mwana wake ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake.
7Asanafe Baasa, Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yehu, mwana wa Hanani, mau omuzenga mlandu Baasa pamodzi ndi banja lake lonse, chifukwa cha zoipa zonse zimene adaachita pamaso pa Chauta. Iyeyo adaputa mkwiyo wa Chauta ndi machimo amene ankachita, olingana ndi a anthu a banja la Yerobowamu, ndiponso chifukwa choti adaaonongeratu banja lonse la Yerobowamu.
Ela mfumu ya ku Israele8Chaka cha 26 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ela mwana wa Baasa adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.
9Tsono munthu wina dzina lake Zimuri, amene anali mkulu woyang'anira hafu la magaleta ake, adamchita chiwembu. Pamene Elayo anali ku Tiriza, namamwa mpaka kuledzera m'nyumba ya Ariza, amene ankayang'anira nyumba yachifumu ku Tirizako,
10Zimuri adadzaloŵa, napha Elayo. Chinali chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Zimuriyo adaloŵa ufumu m'malo mwa Ela.
11Zimuri atangoyamba kulamulira, adapha anthu onse a banja la Baasa. Sadamsiyirepo ndi mwamuna mmodzi yemwe mwa apachibale ake kapena abwenzi ake.
12Motero Zimuri adaononga banja lonse la Baasa monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Yehu mneneri uja. Paja Yehuyo adaadzudzula Baasa
13chifukwa cha zoipa zake ndi za Ela mwana wake, zimene onse aŵiriwo adaachita. Iwo adachimwitsa anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa cha mafano ao.
14Tsono ntchito zina za Ela ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
Zimuri mfumu ya ku Israele15Chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Zimuri adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, koma adangolamulira masiku asanu ndi aŵiri okha. Nthaŵi imeneyo magulu ankhondo a Aisraele adaali akuzinga mzinda wa Gibetoni. Mzindawo unali wa Afilisti.
16Koma pamene ankhondowo adamva kuti Zimuri wachita chiwembu ndipo wapha mfumu, tsiku lomwelo kuzithando komweko onse adasankha Omuri mtsogoleri wankhondo kuti akhale mfumu ya Aisraele.
17Motero Omuri adachoka ku Gibetoni pamodzi ndi ankhondo ake onse, nakazinga mzinda wa Tiriza.
18Zimuri ataona kuti mzinda walandidwa, adathaŵira ku nsanja yam'kati ya nyumba ya mfumu. Adatentha nyumbayo, iye nafera momwemo.
19Adafa choncho chifukwa cha zoipa zake zimene adachita pamaso pa Chauta. Iyeyo ankayenda m'njira zoipa za Yerobowamu, nachimwitsa nazo Aisraele.
20Tsono ntchito zina zonse za Zimuri, ndi chiwembu chimene adachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
Omuri mfumu ya ku Israele21Tsono Israele adagaŵikanso pakati, ena adatsata Tibini mwana wa Ginati, kuti amlonge ufumu, ndipo ena adatsata Omuri.
22Koma anthu otsata Omuri adagonjetsa anthu otsata Tibini, mwana wa Ginati. Choncho Tibini adafa, ndipo Omuri adaloŵa ufumu.
23Chaka cha 31 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Omuri adaloŵa ufumu wa dziko la Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri. Ku Tiriza adalamulirako zaka zisanu ndi chimodzi.
24Iyeyo adagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 zasiliva. Ndipo adamangapo mzinda, namanganso linga kutchinjiriza phirilo. Mzinda umene adaumangawo adautcha Samariya, potsata dzina la Semeri, mwini wake wa phirilo.
25Koma Omuri adachita zoipa pamaso pa Chauta ndipo zoipa zakezo zidaposa za mafumu ena onse akale.
26Ankachita zoipa ngati Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, popembedza mafano.
27Ntchito zina zonse za Omuri zimene ankachita, ndi mphamvu zimene adaonetsa, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
28Ndipo Omuri adamwalira, naikidwa m'manda ku Samariya. Tsono Ahabu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Ahabu mfumu ya ku Israele29Chaka cha 38 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ahabu mwana wa Omuri, adaloŵa ufumu wa ku Israele. Iyeyo adalamulira anthu a ku Israele ku Samariya zaka 22.
30Koma Ahabu adachita zoipa pamaso pa Chauta kupambana mafumu onse akale.
31Adachita ngati sadakhutire ndi kuchimwa konga kwa Yerobowamu, mwakuti adaonjeza tchimo pakukwatira Yezebele, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira fano lotchedwa Baala, ndi kumalipembedza.
32Adamanga nyumba ku Samariya yopembedzeramo Baala,
33ndipo m'nyumbamo adamangamo guwa la Baalayo, naimikamo fano la Asera. Motero Ahabu adachita zinthu zambiri zoputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, kupambana mafumu onse a ku Israele amene adaalipo kale.
34 Yos. 6.26 Pa masiku a mfumu Ahabu, Hiyele wa ku Betele adamanganso mzinda wa Yeriko. Koma monga adaaneneratu Chauta kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni, Abiramu, mwana wamwamuna wachisamba wa Hiyele, adamwalira pa nthaŵi yomanga maziko a mzindawo. Kenaka Segubu, mzime wake, nayenso adamwalira pa nthaŵi yomanga zipata za mzindawo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.