Mas. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yodandaula ndi ina yothokozaKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti: Mbaŵala ya M'maŵa.

1 Mt. 27.46; Mk. 15.34 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?

Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe,

chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga?

2Mulungu wanga, ine ndimalira usana,

koma Inu simundiyankha,

ndimalira usiku, koma sindipeza mpumulo.

3Komabe Inu ndinu oyera,

mumakhala pa mpando wanu waufumu,

ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.

4Makolo athu ankadalira Inu.

Zoonadi, ankakhulupirira Inu,

ndipo Inu munkaŵapulumutsa.

5Ankalirira Inu, ndipo Inu munkaŵalanditsa.

Ankakhulupirira Inu,

ndipo Inu simunkaŵagwiritsa mwala.

6Koma ine ndine nyongolotsi,

sindine munthu konse,

ndine amene anthu onse amandinyodola ndi kundinyoza.

7 Mt. 27.39; Mk. 15.29; Lk. 23.35 Onse ondiwona amandiseka,

amandikwenzulira ndi kupukusa mitu yao.

8 Mt. 27.43 Amati, “Unkadalira Chauta,

Chauta yemweyo akupulumutse.

Akulanditsetu tsono,

popeza kuti amakukonda.”

9Komabe Inu ndinu amene mudalola kuti ndibadwe.

Inu ndinu chikhulupiriro changa,

mudandilera bwino ndili mwana woyamwa.

10Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa,

Inu mwakhala Mulungu wanga

kuyambira pamene mai wanga adandibala.

11Musandikhalire kutali,

pakuti mavuto ali pafupi kundigwera,

ndipo palibe wina wondithandiza.

12Nkhunzi zambiri zandizungulira.

Adani amphamvu ngati nkhunzi za ku Basani andizinga.

13Andiyasamira kukamwa,

ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula.

14Moyo wanga watayika ngati madzi,

mafupa anga aweyeseka.

Mtima wanga uli ngati sera,

wasungunuka m'kati mwanga.

15Kukhosi kwanga kwauma ngati phale,

lilime langa lakangamira ku nsagwada.

Inu mwandisiya pa fumbi kuti ndifere pomwepo.

16Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu.

Aboola manja anga ndi mapazi anga.

17Mafupa anga akuwonekera,

koma anthu aja akungondiyang'anitsitsa

akukondwera poona kuti ndikuvutika.

18 Mt. 27.35; Mk. 15.24; Lk. 23.34; Yoh. 19.24 Agaŵana zovala zanga,

ndipo achitira malaya anga maere.

19Koma Inu Chauta musakhale kutali.

Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.

20Pulumutsani moyo wanga ku lupanga.

Landitseni ku mphamvu za mimbulu.

21Pulumutseni kukamwa kwa mkango,

mulanditse moyo wanga wovutika ku nyanga za njati.

22 Ahe. 2.12 Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu.

Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu.

23Ndidzati,

“Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye.

Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye,

inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.

24“Pakuti sadanyoze munthu wozunzika,

sadaipidwe ndi masautso ake,

sadamubisire nkhope yake,

koma adamumvera pamene adamdandaulira.”

25Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu

chifukwa cha zimene mwandichitira.

Zimene ndidalonjeza ndidzazichita

pamaso pa onse okumverani.

26Ozunzika adzadya ndi kukhuta,

ofunafuna Chauta adzamtamanda.

Ine ndidzati,

“Mitima yanu ikhale ndi moyo nthaŵi zonse.”

27Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi

adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta,

mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza.

28Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta,

Iye amalamula anthu a mitundu yonse.

29Anthu onse odzitama adzamuŵeramira.

Anthu onse oloŵa m'manda nawonso adzamugwadira,

ndiye kuti onse osatha kudzisungira moyo.

30Zidzukulu zam'tsogolo zidzatumikira Ambuye.

Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye.

31Adzalalika za chipulumutso chake

kwa anthu amene mpaka tsopano sanabadwe,

ponena kuti Chauta ndiye adapulumutsa anthu ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help