1 Mbi. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zidzukulu za Yuda

1Ana a Yuda naŵa: Perezi, Hezironi, Karimi. Huri ndi Sobala.

2Reaya mwana wa Sobala adabereka Yahati, Yahati adabereka Ahumai ndi Lahadi. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Azorati.

3Ana a Huri naŵa: Etamu amene adabereka Yezireele, Isima ndi Idibasi, ndiponso mlongo wao Hazeleleponi;

4Penuwele amene adabereka Gedori ndi Ezere amene adabereka Husa. Ameneŵa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi tate wa Betelehemu.

5Asuri amene adabereka Tekowa, anali ndi akazi aŵiri, Hela ndi Nara.

6Nara adamubalira Ahuzamu, Hefere, Temeni, ndi Haahasitari. Ameneŵa ndiwo anali ana a Nara.

7Ana a Hela naŵa: Zereti, Izara ndi Etinani.

8Kozi adabereka Anubu, Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele, mwana wa Harumu.

9Panali munthu wina dzina lake Yabezi amene anthu ankamlemekeza kupambana abale ake. Mai wake pomutcha dzina la Yabezi ankanena kuti, “Chifukwa ndidamubala movutikira.”

10Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.

Maina ena a mabanja

11Kelubi, mbale wa Suha, adabereka Meiri, Meiri adabereka Esitoni.

12Esitoni adabereka Beterafa, Paseya ndi Tehina, tate wa Irinahasi. Ameneŵa ndiwo anthu a ku Reka.

13Ana a Kenazi naŵa: Otiniyele ndi Seraya. Ana a Otiniyele naŵa: Hatati ndi Meonotai.

14Meonotai adabereka Ofura. Ndipo Seraya adabereka Yowabu, tate wa Ageharasimu. Adaŵatcha choncho popeza kuti anali anthu azaluso.

15Ana a Kalebe, mwana wa Yefune, naŵa: Iru, Ela, ndi Naamu. Mwana wa Ela anali Kenazi.

16Ana a Yehalelele naŵa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asarele.

17Ana a Ezara naŵa: Yetere, Meredi, Efere ndi Yaloni. Meredi adakwatira Bitiya, mwana wa Farao. Mkaziyo adatenga pathupi nabala Miriyamu, Samai ndi Isiba, bambo wa Esitemowa.

18Tsono mkazi wake Wachiyuda adamubalira Yeredi, bambo wa Gedori, Hebere bambo wa Soko, ndiponso Yekutiyele bambo wa Zanowa.

19Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo adabereka Keila Mgarimi ndiponso Esitemowa Mmaakati.

20Ana a Simoni naŵa: Aminoni, Rina, Benihanani ndi Tiloni. Ana a Isi naŵa: Zoheti, ndi Benizoheti.

Zidzukulu za Sela

21Ana a Sela, mwana wa Yuda, naŵa: Eri, tate wa Leka, Laada, tate wa Maresa ndi wa mabanja a anthu oomba nsalu zabafuta ku Betasebea.

22Kunalinso Yokimu, pamodzi ndi amuna a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi amene ankalamula ku Mowabu, koma adabwerera ku Lehemu (tsono nkhani zimenezitu nzakalekale).

23Ameneŵa anali anthu oumba mbiya ndiponso nzika za ku Netaimu ndi ku Gedera. Adakhala kumeneko pamodzi ndi mfumu, namaigwirira ntchito.

Zidzukulu za Simeoni

24Ana a Simeoni naŵa: Nemuwele, Yamini, Yaribu, Zera ndi Shaulo.

25Salumu anali mwana wake, kudzanso Mibisamu ndi Misima.

26Ana a Misima naŵa: Hamuele kudzanso Zakuli ndi Simei.

27Simei anali nawo ana aamuna 16, ndi ana aakazi asanu ndi mmodzi. Koma abale ake analibe ana ambiri, ndipo mabanja ao sadakule kufanana ndi anthu a ku Yuda.

28Yos. 19.2-8 Iwowo ankakhala ku Beereseba, Molada, Hazara-Suwala,

29Biliha, Ezemu, Toladi,

30Betuele, Horoma, Zikilagi,

31Betemara-Kaboti, Hazara-Susimu, Betebiri ndiponso ku Saaraimu. Imeneyi inali mizinda yao mpaka nthaŵi imene Davide adayamba kulamulira.

32Ndipo midzi yao inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, mizinda isanu,

33pamodzi ndi midzi yao ina yozungulira mizinda imeneyi, mpaka kukafika ku Baala. Kumeneku ndiko kumene ankakhala ndipo ankasunga mndandanda wa maina.

34Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya,

35Yowele, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele,

36Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaiya, Adiyele, Yesimiele, Benaya,

37Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri ndiponso mwana wa Semaya.

38Anthu amene tatchulaŵa ndiwo anali atsogoleri a mabanja ao, ndipo mabanja a makolo ao adaonjezeka kwambiri.

39Motero adapita cha kunja kwa mudzi wa Gedori, kuvuma kwa chigwa, kuti akafunefune busa la ziweto zao.

40Kumeneko adakapezako busa lokoma ndi la msipu wambiri. Dziko lakenso linali lalikulu, labata ndi laufulu. Anthu amene ankakhala kumeneko kale anali Ahamu.

41Anthu a fuko a Simeoniwo, ochita kulembedwa maina, adadza pa nthaŵi ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, ndipo adaononga mahema a Ahamuwo ndi kupha Ameuni amene adaŵapeza kumeneko. Adaonongeratu anthu onsewo kotero kuti dzina lao silidamvekenso mpaka lero lino. Kenaka iwowo adakhala ku malo amenewo, popeza kuti kunali msipu womadyetsako ziweto zao.

42Asimeoni ena okwanira mazana asanu, adapita ku phiri la Seiri. Atsogoleri ao anali Pelatiya, Neyariya, Refaya ndi Uziyele, ana a Isi.

43Iwowo adaononga Aamaleke otsala amene anali atapulumuka, ndipo adakhala kumeneko mpaka lero lino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help