Mas. 86 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Salmo lopempha chithandizoPemphero la Davide.

1Tcherani khutu, Inu Chauta, ndipo mundiyankhe,

pakuti ndine wosauka ndi wosoŵa.

2Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu.

Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu.

Inu ndinu Mulungu wanga.

3Mundikomere mtima, Inu Ambuye,

popeza kuti ndimalirira Inu tsiku lonse.

4Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu,

pakuti ndikupereka mtima wanga kwa Inu Ambuye.

5Inu Ambuye ndinu abwino,

ndipo mumakhululukira anthu anu.

Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu

kwa onse amene amakupembedzani.

6Tcherani khutu, Inu Chauta,

kuti mumve pemphero langa.

Mverani kulira kwanga kopemba.

7Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani,

pakuti mumayankha mapemphero anga.

8Pakati pa milungu palibe ndi mmodzi yemwe

wolingana nanu, Inu Ambuye,

palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.

9 Chiv. 15.4 Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera,

idzakuŵeramirani, Inu Ambuye,

ndipo idzalemekeza ukulu wanu.

10Pakuti Inu ndinu wamkulu,

mumachita zinthu zodabwitsa,

Inu nokha ndinu Mulungu.

11Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta,

kuti ndiziyenda m'zoona zanu.

Mundipatse mtima wosagaŵikana,

kuti ndiziwopa dzina lanu.

12Inu Ambuye, Mulungu wanga,

ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse,

ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.

13Paja chikondi chanu chosasinthika kwa ine nchachikulu,

Mwandipulumutsa ku malo akuya a anthu akufa.

14Inu Mulungu, anthu achipongwe andiwukira.

Anthu opanda chifundo akufunafuna moyo wanga

ndipo sasamala za Inu.

15Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo

ndinu Mulungu wokoma mtima,

wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika,

ndi wokhulupirika kotheratu.

16Mundiyang'ane ndipo mundichitire chifundo.

Mundipatse mphamvu zanu ine mtumiki wanu,

mundipulumutse ine mwana wa mdzakazi wanu.

17Mundiwonetse chizindikiro chakuti mumandikomera mtima,

kuti odana nane achite manyazi.

Adzaona kuti Inu Chauta mwandithandiza

ndi kundilimbitsa mtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help