1Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.
2Musanayambe kumenya nkhondo, wansembe abwere, ndipo auze ankhondowo kuti,
3“Imvani, inu Aisraele! Lero mukuyamba kumenya nkhondo ndi adani anu. Musataye mtima ai! Musaŵaope adaniwo, musanjenjemere, musachite mantha.
4Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”
5Pamenepo akuluakulu a ankhondo adzauza anthu kuti, “Kodi alipo pano munthu amene wangomanga nyumba yatsopano, koma sanaipereke kwa Mulungu? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzaipereka nyumbayo.
6Kodi alipo pano wina amene wangooka mipesa m'munda, koma osakhala ndi mwai woti nkuthyola mphesa zake? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzamwe vinyoyo.
7Kodi alipo wina pano amene adafunsira mbeta koma mkaziyo sanaloŵane naye? Ngati alipo, abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzakwatire mbetayo.”
8Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.”
9Akuluakulu atamaliza kulankhula ndi gulu lankhondolo, asankhe mtsogoleri pa gulu lililonse.
10Mukamapita kukathira nkhondo mzinda, poyamba apatseni anthu amumzindawo mwai woti agonje okha.
11Akakutsekulirani zipata nakugonjerani, akhale akapolo anu onsewo, ndipo akugwirireni ntchito yaukapolo.
12Koma ngati anthu a mu mzinda umenewo akana kugonja, nasankhula nkhondo, uzingeni mzindawo ndi gulu lanu lankhondo.
13Chauta, Mulungu wanu, akakulolani kugonjetsa mzindawo, muphe mwamuna aliyense m'menemo.
14Koma akazi ndi ana mungoŵagwira, ndipo mutengenso zoŵeta ndi zonse zimene zili mumzindamo ngati zofunkha zanu. Zinthu zonse za adani anu muzigwiritse ntchito, Chauta wakupatsani zimenezo.
15Umu ndi m'mene muzikachitira ndi mizinda ya kutali ndi inu, imene siili mizinda ya anthu akuno.
16Koma mukadzalanda mizinda imene ili m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, muphe aliyense.
17Muŵaononge kotheratu onse anthu aŵa: Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi, monga momwe Chauta Mulungu wanu adakulamulirani.
18Iphani onse, kuti angadzakuchimwitseni kuchimwira Chauta, Mulungu wanu, pokuphunzitsani zoipa zimene iwowo amachita akamapembedza milungu yao.
19Pamene muzinga mzinda nthaŵi yaitali ndi cholinga choti muulande, musagwetse mitengo yake yazipatso, mungathe kudya zipatso zake, koma mitengo yake musagwetse, chifukwa adani anu si mitengoyo.
20Koma mitengo ina yosabereka zipatso mungathe kuidula ndi kumagwira nayo ntchito popanga makina ankhondo okhalirira mzinda umene mukulimbana nawo mpaka mutaugonjetsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.