1Mose adayankha kuti, “Koma Aisraelewo sakandikhulupirira, kapena kumvera mau anga. Adzati, ‘Chauta sadakuwonekere.’ ”
2Chauta adafunsa Moseyo kuti, “Kodi nchiyani chili m'manja mwakocho?” Mose adayankha kuti, “Ndodo.”
3Chauta adamuuza kuti, “Taiponya pansi.” Mose ataiponya pansi ndodoyo, idasanduka njoka, iye nkuithaŵa njokayo.
4Apo Chauta adauza Mose uja kuti, “Igwire mchira.” Mose adaigwira, pompo idasandukanso ndodo m'manja mwakemo.
5Chauta adamuuza kuti, “Ukachite zimenezi, ndipo adzakhulupirira kuti Chauta, Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, adakuwonekeradi.”
6Chauta adauzanso Mose kuti, “Tapisa dzanja lako m'malayamo.” Iye adapisadi. Koma potulutsa dzanjalo, linali lakhate, lotuŵa ngati ufa.
7Tsono Chauta adati, “Lipisenso m'malayamo dzanja lakolo.” Iye adalipisanso ndipo potulutsa, linali labwinobwino lopanda khate, koma lofanana ndi thupi lake lonse.
8Pamenepo Chauta adati, “Akakapanda kukukhulupirira, osasamala chizindikiro choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chizindikiro chachiŵiricho.
9Koma akakapanda kukhulupirira zizindikiro ziŵiri zonsezo, osafuna kumva zomwe ukaŵauzezo, ukatenge madzi a mu mtsinje wa Nailo, ukaŵathire pa nthaka youma. Madzi amenewo akasanduka magazi.”
10Mose adati, “Pepani Chauta, ndapota nanu, ine sindidziŵa kulankhula bwino chiyambire kale, kapena kuyambira paja mwayamba kulankhula nane mtumiki wanune. Lilime langa ndi lolemera, ndine wachibwibwi.”
11Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi adapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosamva kapena wosalankhula, wopenya kapena wosapenya? Kodi si ndine Chauta amene ndimachita zimenezo?
12Tsono pita, Ine ndidzakuthandiza kulankhulako, ndipo zoti ukanene ndidzakuuza ndine.”
13Koma Mose adati, “Pepani Chauta, ndikukupemphani kuti mutume wina amene angathe kulankhula bwino.”
14Pompo Chauta adamkalipira Mose, namufunsa kuti, “Bwanji mbale wako Aroni, Mlevi uja? Ndikudziŵa kuti angathe kulankhula bwino kwambiri. Iyeyo akubwera kudzakumana nawe, ndipo adzakondwa kwambiri pokuwona.
15Udzalankhula naye iyeyo ndi kumuuza zoti akanene. Ndidzakuthandizani kulankhula nonse aŵirinu, ndipo ndidzakuuzaninso zoti mukachite.
16Iye azikalankhula kwa anthu m'malo mwako. Adzakhala wokulankhulira, ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu ndiwe kwa Aroni.
17Utenge ndodo ili m'manja mwakoyo, ukachite nayo zozizwitsa ndodo imeneyo.”
Mose abwerera ku Ejipito18Tsono Mose adabwerera kwa Yetero mpongozi wake uja, namuuza kuti, “Chonde mundilole kuti ndibwerere ku Ejipito kwa abale anga, kuti ndikaŵaone ngati ali moyo.” Yetero adauza Mose kuti, “Pitani ndi mtendere.”
19Chauta adauza Mose ku Midiyani kuja kuti, “Bwerera ku Ejipito tsopano popeza kuti onse aja ankafuna kukuphaŵa adamwalira.”
20Motero Mose adatenga mkazi wake ndi ana ake, naŵakweza pa bulu onsewo, ndipo adapita ku Ejipito, atatenga ndodo imene adampatsa Mulungu ija.
21Chauta adauzanso Mose kuti, “Pamene ukubwerera ku Ejipito, ukachite ndithu pamaso pa Farao zozizwitsa zonse zimene ndakuuza kuti ukachite. Koma ndidzamuumitsa mtima, ndipo sadzalola kuti anthu anga apite.
22Ndipo ukamuuze Farao kuti, Ine Chauta ndikuti Israele ali ngati mwana wanga wachisamba.
23 mwa Mose. Kenaka Ziporayo adati, “Zoonadi, iwe ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi.”
26Choncho Chauta adamleka Mose osamupha. Ndiye pamene Zipora adanena kuti, “Ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi,” chifukwa cha kuumbalako.
27Chauta adauza Aroni kuti, “Pita ku chipululu kuti ukakumane ndi Mose.” Aroni adapitadi kukakumana naye ku phiri la Mulungu, namumpsompsona.
28Pamenepo Mose adafotokozera Aroni zonse zimene Chauta adaamuuza, pa nthaŵi imene ankamutuma. Adamuuzanso za zozizwitsa zonse zija zimene Chauta adamlamula kuti akachite.
29Motero Mose ndi Aroni adapita, nakasonkhanitsa atsogoleri onse a Aisraele.
30Aroni adafotokozera atsogoleriwo zonse zimene Chauta adaauza Mose, ndipo adachita zozizwitsa zonse zija anthuwo akupenya.
31Pamenepo Aisraele aja adakhulupiriradi zimenezo. Tsono atamva kuti Chauta adadzaŵayendera ndipo kuti adaona kuzunzika kwaoko, adaŵeramitsa mitu pansi napembedza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.