1Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse.
2Popeza kuti si ana anu, koma ndinu amene mudazidziŵa ndi kuziwona zakale zonsezo, mukumbukire za Chauta, Mulungu wanu. Ukulu wake mudauwona, mudaonanso dzanja lake lamphamvu ndi mkono wake wotambalitsa.
3 kuti aŵaphimbe ndi kuŵaononga onsewo.
5Mudaona zonse zimene Chauta adakuchitirani m'chipululu muja, musanafike kuno.
6Num. 16.31, 32 Mudaona zimene Chauta adachita pa Datani ndi pa Abiramu, ana a Eliyabu, a fuko la Rubeni. Pamaso pa Aisraele onse nthaka idatsekuka nkuŵakwirira anthuwo, pamodzi ndi a m'banja mwao, mahema ao ndi zoŵeta zao zomwe.
7Zoonadi mudaona zazikulu zonse zimene Chauta adachita.
Madalitso m'dziko lachilonjezo8Muzimvera zonse zimene ndakulamulani lerozi. Tsono mukatero, mudzakhala amphamvu, ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dzikomo.
9Mudzakhaladi nthaŵi yaitali m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta adalumbira kuti adzapatsa makolo anu ndi zidzukulu zao.
10Dziko limene mukukakhalamolo likusiyana ndi dziko la Ejipito kumene mudachokera. Kumene kuja munkati mukafesa mbeu zanu, munkachita kuthirira ngati m'madimba.
11Koma dziko limene mukukaloŵamolo ndi lamapiri ndi lazigwa. M'dziko limenelo mvula siitha.
12Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene amasamalira dziko limenelo ndi kumaliyang'anira chaka chonse mosalekeza.
13 Lev. 26.3-5; Deut. 7.12-16; 28.1-14 Nchifukwa chake tsono muzimvera malamulo ndakupatsani leroŵa: kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
14Ndipo Iye azidzagwetsa mvula m'dziko mwanu pa nthaŵi yake, monga nthaŵi yadzinja ndiponso nthaŵi yachilimwe, kotero kuti mudzakhala ndi tirigu wambiri, vinyo wambiri ndiponso mafuta aolivi ambiri.
15Adzameretsa udzu woti ng'ombe zanu zizidzadya, ndipo inunso mudzapeza chakudya ndi kukhuta.
16Chenjerani, musasokeretsedwe ndi kutembenukira kwa milungu ina, kuti muziipembedza ndi kuitumikira,
17chifukwa Chauta adzakukwiyirani, adzakumanani mvula, ndipo nthaka sidzabalanso zipatso zake. Motero mudzaonongeka msanga m'dziko lokomali limene Chauta akukupatsani.
18 Deut. 6.6-9 Malamulo ameneŵa akhale m'mitima mwanu ndi m'maganizo mwanu. Muŵamange pamikono panu ndi pa mphumi pakati pa maso anu, kuti akhale chikumbutso.
19Muŵaphunzitse kwa ana anu. Muziphunzitsa mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
20Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa makomo anu.
21Pamenepo inu ndi ana anu, mudzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adalumbira kuti adzapatsa makolo anu. Mudzakhala m'dziko limenelo nthaŵi zonse.
22Muzimvera mokhulupirika zonse zimene ndakuuzanizi. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zonse zimene akulamulani, ndipo mukhale okhulupirika kwa Iye.
23Tsono pamene inu mukupita, Chauta adzapirikitsa mitundu ina yonseyo, ndipo mudzalanda maiko a mitundu ya anthu akuluakulu ndi amphamvu kupambana inu.
24Yos. 1.3-5 Nthaka yonse imene mupondepoyo idzakhala yanu. Dziko lanulo lidzayambira ku chipululu kumwera, mpaka ku phiri la Lebanoni kumpoto, ndiponso kuyambira ku mtsinje wa Yufurate kuvuma, mpaka ku Nyanja Yaikulu kuzambwe.
25Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adzakuletseni. Kulikonse kumene mudzapite m'dziko limenelo, anthu azidzakuwopani, monga momwe Mulungu wakulonjezerani kuti adzaŵachititsa mantha anthu amenewo.
26Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero.
27Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa.
28Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
29Deut. 27.11-14; Yos. 8.33-35 Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limene mukupita kukakhalamolo, muzikalalika madalitso ameneŵa mutakwera pa phiri la Gerizimu, koma matembereroŵa muzikaŵalalika mutakwera pa phiri la Ebala.
30Mapiri aŵiri ameneŵa ali chakuzambwe kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, m'dziko la Akanani amene amakhala m'chigwa cha Yordani, pafupi ndi mitengo ya thundu ya ku More, kuyang'anana ndi Giligala.
31Muli pafupi kuwoloka Yordani ndi kukakhalamo m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani. Mukakalilandira ndi kukhalamo,
32mukasamale kumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani leroŵa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.