Mphu. MAU OYAMBIRIRA - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

MAU OYAMBIRIRAMaphunzitso akuluakulu ambiri adatifikira mwa njira ya Malamulo ndi Aneneri ndi enanso obwera pambuyo pao. Tsono nkoyenera kuŵatamanda Aisraele chifukwa cha maphunzitso aowo ndi nzeru zaozo. Koma nkosakwanira kuti oŵerenga maphunzitsowo angopezamo nzeru za iwo okha. Nkofunikanso ndithu kuti anthu amene ali ndi chidwi pophunzira, azithandiza anzao ena poŵaphunzitsa ndi mau apakamwa ndiponso zolemba zao.Agogo anga aYesu ankachita khama kuŵerenga Malamulo ndi Aneneri ndi mabuku ena amene makolo athu adatisiyira, ndipo adaphunziradi zambiri. Tsono nawonso adafuna kulemba zina za malangizo ndi za nzeru, kuti anthu okonda kuphunzira akaŵerenga zimenezi, azisunthira m'tsogolo potsatadi Malamulo pa moyo wao.Ndiye ndikukupemphani kuti muziŵerenga bukuli ndi mtima wofuna kuphunzira ndiponso mosamala kwambiri. Ngati paoneka kuti tidalephera pena ndi pena kunena bwino zimene mauwo amatanthauza, apo mutikhululukire. Mau ena achihebri nkovuta kuŵapezera tanthauzo lake lenileni m'chilankhulo china. Zimenezi zimaoneka osati m'buku lino lokha, komanso m'mabuku a Malamulo ndi a Aneneri ndi mabuku ena. Choncho pamapezeka zina zosiyana kwambiri ndi zomwe zidalembedwa m'chilankhulo choyamba.Tsono pa chaka cha 38 cha ufumu wa Ptolemeyo Evergetesi, ndidafika ku Ejipito. Ndipo nditakhalako nthaŵi, ndidapezako buku la malangizo aakulu. Choncho ndidaaganiza kuti nkwabwino kuti nditanganidwe ndi ntchito yotanthauza buku limeneli. Ndipo ndidalimbikira masiku ambiri kulisanduliza mosamala, mpaka kutsiriza. Ndinkafuna kuti alitulutse ndi kulitumiza kwa anthu okhala m'maiko akunja, amene ankafuna kuwonjezera pa maphunziro ao, ndipo anali okonzeka kutsata Malamulo pa moyo wao.Mau oyambiriraŵa ndi a mlembi chabe, angofotokoza za m'mene adaganizira kuika pamodzi malangizo ochokera kwa agogo ake aYesu, amene anali mwana wa Sira.
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help