1Saulo adalamula mwana wake Yonatani ndi akuluakulu onse kuti aphe Davide. Koma Yonatani ankakonda Davide kwambiri.
2Choncho adakauza Davide kuti, “Iwe, abambo anga akufuna kukupha. Ndiye uchenjere, m'maŵa ukakhale kwina kobisalika.
3Ine ndidzapita ndi kukaima pakhundu pa bambo wanga kuminda kumene iwe ukabisaleko, tsono ndidzalankhula ndi bambo wanga za iwe. Chilichonse chimene ndidzamve, ndidzakuuza.”
4Tsono Yonatani adaterodi ndipo adakanena zabwino za Davide kwa bambo wake, namuuza kuti, “Atate, musachimwire mtumiki wanu Davide, poti sadakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino.
5Paja adaaika moyo wake pa minga pakupha Goliyati Mfilisti uja. Pambuyo pake Chauta adachita zazikulu pakupambanitsa Aisraele pa nkhondo. Inu mudaona zimenezo ndi kukondwera nazo. Chifukwa chiyani tsono mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa, pofuna kumupha Davideyu?”
6Saulo adamvera mau a Yonatani, ndipo adalumbira kuti, “Mulungudi! Davideyo sadzaphedwa!”
7Tsono Yonatani adaitana Davide namuuza zonsezo. Choncho Yonatani adabwera naye kwa Saulo, ndipo Davideyo ankatumikira Saulo monga kale.
8Nkhondo ina idabukanso. Davide adapita kukamenyana ndi Afilisti. Adapha Afilisti ambiri, kotero kuti iwowo adathaŵa.
9Tsiku lina mzimu woipa uja udatsikira Saulo pa nthaŵi yomwe anali m'nyumba mwake, mkondo uli m'manja, Davide akuimba zeze.
10Pomwepo Saulo adayesa kubaya Davide ndi kumkhomera ku chipupa. Koma Davide adauleŵa mkondowo, kotero kuti udangolasa chipupa. Ndipo adathaŵa napulumuka.
11 Mas. 59 Usiku womwewo Saulo adatuma anthu kunyumba kwa Davide kuti akambisalire, kuti choncho akamuphe Davide m'maŵa. Koma Mikala, adauza mwamuna wake Davide kuti, “Mukapanda kupulumutsa moyo wanu usiku uno, maŵa muphedwa.”
12Choncho Mikala adamtulutsira Davideyo pa windo, ndipo adathaŵa.
13Mikalayo adatenga fano lam'nyumba naligoneka pa bedi, naika mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo, nalifunditsa nsalu.
14Pamene anthu a Saulo aja adafika kuti adzamgwire Davide, Mikala adati, “Davide akudwala.”
15Koma Saulo adaŵatumanso anthuwo kuti akamgwire ndithu Davideyo. Adaŵauza kuti, “Mubwere naye kuno, mumnyamulire pabedi pomwepo kuti ndidzamuphe.”
16Anthuwo atakaloŵa, adangoona fano pabedipo ndi mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo.
17Atamva zimenezi Saulo adafunsa Mikala kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga chotere pa kulola kuti mdani wanga athaŵe?” Mikala adayankha kuti, “Davide adaandiwuza kuti, ‘Undilole ndipite. Ngati sutero, ndikupha.’ ”
18Choncho Davide adathaŵa napulumuka, nakafika kwa Samuele ku Rama. Adafotokozera Samuele zonse zimene Saulo adamuchita. Tsono Davideyo pamodzi ndi Samuele adakakhala ku Nayoti.
19Saulo atamva kuti Davide ali ku Nayoti ku Rama,
20pompo adatumanso anthu kuti akamgwire. Anthuwo adaona gulu la aneneri akuvina namalosa, Samuele akuŵatsogolera. Pamenepo mzimu wa Mulungu udaŵaloŵa anthuwo ndipo nawonso adayamba kulosa.
21Saulo atazimva zimenezo, adatuma anthu ena, ndipo nawonso adayamba kulosa. Adatumanso anthu ena kachitatu, nawonso adayamba kulosa.
22Choncho Saulo mwini wake adanyamuka napita ku Rama, nakafika pa chitsime chachikulu chimene chili ku Seku. Ndipo adafunsa kuti, “Kodi Samuele ndi Davide ali kuti?” Munthu wina adati, “Ali ku Nayoti ku Rama.”
23Saulo adachoka napita ku Nayoti ku Rama. Nayenso mzimu wa Mulungu udamloŵa ndipo ankayenda akuvina namalosa mpaka kukafika ku Nayoti ku Rama.
241Sam. 10.11, 12Nayenso adavula zovala zake namalosa pamaso pa Samuele, kenaka nkugona chamaliseche tsiku lonse, usana ndi usiku. Choncho padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.