2 Maf. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hoseya mfumu ya ku Israele

1Chaka cha 12 cha ufumu wa Ahazi mfumu ya ku Yuda, Hoseya mwana wa Ela adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zinai.

2Tsono adachita zoipa kuchimwira Chauta, komabe osalingana ndi mafumu a ku Israele amene ankalamulira, iyeyo asanaloŵe ufumu.

3Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adadza kudzamthira nkhondo, ndipo Hoseya adamgonjera, namakhoma msonkho kwa iyeyo.

4Koma tsiku lina mfumu ya ku Asiriya idaona kuti Hoseya akuchita zaupandu. Ndiye kuti Hoseyayo anali atatuma amithenga kukapempha chithandizo kwa So, mfumu ya ku Ejipito, Ndiponso adaaleka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, m'menemo kale ankakhoma chaka ndi chaka. Nchifukwa chake mfumu ya ku Asiriya itamva zimenezi, idamanga Hoseya ndi kumuika m'ndende.

Kupasuka kwa mzinda wa Samariya

5Nthaŵi yomweyo Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adathira nkhondo dziko la Israele nakafika ku Samariya, nkukauzinga mzindawo ndi zithando zankhondo zaka zitatu.

6Chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwao kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi.

7Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m'manja mwa Farao mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina,

8ndipo ankayenda motsata miyambo ya anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pamene ankafika Aisraele. Ankatsatanso miyambo yachilendo imene mafumu ena a Aisraele anali ataiyambitsa.

9Ndipo Aisraele ankachita zinthu zoipa mobisika namachimwira Chauta Mulungu wao. Adadzimangira akachisi opembedzerako mafano ku midzi yao yonse ndi ku mizinda yomwe.

10 m'malo mwa Aisraele amene adatengedwa ukapolo. Tsono anthuwo adaloŵa m'midzi ya Samariyayo naisandutsa yaoyao.

25Koma iwowo chiloŵere chao kumeneko sankapembedza Chauta. Nchifukwa chake Chauta adatumiza mikango pakati pao, nipha ena mwa iwowo.

26Motero mfumu ya ku Asiriya idamva kuti, “Anthu a mitundu ina aja amene mudaŵakhazika m'midzi ya ku Samariya, sakudziŵa kupembedza Mulungu wa dzikolo. Nchifukwa chake Mulungu adaŵatumizira mikango pakati pao, ndipo ikuŵapha, chifukwa sakuchita zimene Mulunguyo akufuna.”

27Tsono mfumu ya ku Aasiriya idalamula kuti, “Tumani mmodzi mwa ansembe amene mudaŵagwira kumeneko, akakhale komweko, kuti akaŵaphunzitse kupembedza Mulungu wa dzikolo.”

28Motero mmodzi mwa ansembe amene adaŵatenga ku Samariya adadzakhala ku Betele, nayamba kuŵaphunzitsa anthu kupembedza Chauta.

29Koma mtundu uliwonse wa anthuwo unkapangabe mafano a milungu yaoyao, ndipo ankaika milunguyo m'nyumba zachipembedzo zimene Asamariya adaazimanga. Mtundu uliwonse wa anthuwo unali ndi nyumba za mulungu wao ku mzinda uliwonse kumene ankakhala.

30Anthu a ku Babiloni adadzipangira fano lotchedwa Sukoti-Benoti. Anthu a ku Kuta adapanga fano lotchedwa Neregali, anthu a ku Hamati adapanga fano lotchedwa Ashima.

31Aavi adapanga fano lotchedwa Nibihazi ndiponso Taritaki. Asefaravaimu ankapereka ana ao ngati nsembe zopsereza kwa Adrameleki ndi kwa Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

32Anthuwo ankapembedzanso Chauta nadzisankhira pakati pao anthu wamba, kuti akhale ansembe otumikira ku nyumba zao zachipembedzo. Ansembe amenewo ndi amene ankaperekera anthu nsembe m'nyumba zopembedzeramo milungu yao ku zitunda.

33Motero ankapembedza Chauta, kwinaku ankatumikirabe milungu yao, potsata makhalidwe a mitundu ya anthu a kumene adatengedwa ukapoloko.

34Gen. 32.28; 35.10Akuchitabe zimene ankachita kale mpaka lero lino.

Iwowo salemekeza Chauta kwenikweni ndipo satsata zogamula kapena zolengeza, ngakhale malangizo kapena malamulo amene Chauta adalamula zidzukulu za Yakobe, amene adamtchula kuti Israele.

35Eks. 20.5; Deut. 5.9 Chauta adaachita nawo Aisraele chipangano naŵalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuilambira kapena kuitumikira, kapena kuiperekera nsembe.

36Deut. 6.13 Koma muzipembedza Ine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito ndi mphamvu zanga zazikulu ndi mkono wanga wokutetezani. Muzigwadira Ine Chauta, ndipo muzipereka nsembe kwa Ine ndekha.

37Ndipo inu muzisamala zogamula ndi zolengeza, malangizo ndi malamulo amene Ine Chauta ndidakupatsani. Musamapembedza milungu ina ai,

38ndipo musaiŵale chipangano chimene ndidachita ndi inu. Musamapembedze milungu ina,

39koma muzipembedza Ine Chauta Mulungu wanu, ndipo ndidzakupulumutsani kwa adani anu.”

40Komabe iwowo sankamva zimenezi, koma ankachitabe zimene adakhala akuchita kuyambira kale.

41Motero mitundu ya anthu imeneyi inkapembedza Chauta, kwinaku nkumatumikira milungu yao yachabechabe ija. Ana ao adachitanso zomwezo, adzukulu ao adachita zokhazokhazo zimene ankachita makolo ao, ndipo akuchitabe zomwezo mpaka pano.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help