1 Am. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Gorjiyasi adatenga ankhondo oyenda pansi 5,000, ndi okwera pa akavalo chikwi chimodzi odziŵa nkhondo zedi, nkuyenda nawo usiku.

2Adapita kukathira nkhondo magulu ankhondo a Ayuda ndi kuŵakantha modzidzimutsa. Alonda a ku boma lankhondo ndiwo ankaŵatsogolera.

3Koma Yudasi atamva zimenezo, adapita ndi ankhondo ake onse kukamenyana ndi ankhondo a mfumu amene anali ku Emausi.

4Nthaŵi yomweyo nkuti gulu lankhondo la Gorjiyasi lija kudakalibe ku zithando zao zankhondo.

5Gorjiyasi atakafika ku zithando zankhondo za Yuda usiku, sadapezeko munthu ndi mmodzi yemwe. Tsono adayamba kukaŵafunafuna ku mapiri, chifukwa mumtima mwake ankati, “Ayudaŵa akutithaŵa.”

6Kutacha, Yudasi adatulukira m'chigwa pamodzi ndi anthu zikwi zitatu, koma analibe malaya ankhondo kapena malupanga okwanira, monga m'mene ankafunira.

7Adaona zithando zankhondo za anthu akunja zili zolimba ndi zozingidwa ndi malinga, ndipo ankhondo okwera pa akavalo atazizungulira, onse odziŵa kumenya nkhondo.

8Komabe Yudasi adauza anthu ake kuti, “Musaope kuchuluka kwao, musachite mantha akayamba kutigudukira.

9Kumbukirani m'mene makolo athu adapulumukira ku Nyanja Yofiira pamene paja Farao adaaŵalondola ndi ankhondo ake.

10Tsopano tiyeni tipemphere kwa Mulungu Kumwamba. Tipemphe kuti atikomere mtima, akumbukire chipangano chake chimene adachita ndi makolo athu, ndipo aononge gulu lankhondo lili panoli.

11Pamenepo anthu onse a mitundu ina adzadziŵa kuti alipodi Wopulumutsa ndi Woombola Aisraele.”

12Anthu achilendo aja poyang'ana, adaona Ayuda alikudza kudzaŵathira nkhondo.

13Tsono iwowo adatuluka ku zithando zao kudzamenyana nawo nkhondo. Pamenepo Yudasi ndi anthu ake adaliza malipenga naŵayandikira.

14Adayamba kumenyana nkhondo. A mitundu ina aja adagonjetsedwa nkuthaŵira ku chigwa.

15Ankhondo ao onse am'mbuyo adaphedwa ndi lupanga. Tsono Yudasi adaŵalondola mpaka ku Gazara, ku zigwa za Idumeya, ku Azoto ndi ku Yaminiya. Adani okwanira zikwi zitatu adaphedwa.

16Apo Yudasi ndi ankhondo ake adaleka kuŵalondola nabwerera. Iye adauza anthu ake kuti,

17“Musathamangire zofunkha, chifukwa kuli inansotu nkhondo kutsogoloku.

18Gorjiyasi ndi ankhondo ake ali ku mapiri pafupi nafe. Tsono chitani chamuna tsopano, mumenyane nawo adani athu, ndipo bwino lino mudzafunkha chuma chao.”

19Yudasi akulankhulabe, ankhondo ena a Gorjiyasi adatulukira kuchokera ku mapiri.

20Iwowo adaaona kuti anzao athaŵa, ndipo zithando zao zilikupsa, chifukwa kumeneko utsi unali tolotolo.

21Poona utsiwo adachita mantha kwambiri. Pamenenso adaona m'chigwamo ankhondo a Yuda ali okonzeka kumenyana nawo nkhondo,

22onse adathaŵira ku dziko la Afilisti.

23Yudasi ndi ankhondo ake adabwerera kukafunkha chuma ku zithando zankhondo za adani. Adatenga golide ndi siliva wochuluka, nsalu zobiriŵira ndi zofiirira ndi chuma chambiri.

24Pobwerako Ayuda ankaimba nyimbo zothokoza ndi kuyamika Mulungu. Ankati, “Mulungu ngwabwino, ndipo chifundo chake nchamuyaya!”

25Choncho tsiku limenelo linali la chipulumutso chachikulu kwa Aisraele.

26Ankhondo achilendo amene adaathaŵa aja, adakadziŵitsa Lisiyasi zimene zidachitika.

27Atamva zimenezi, iye adavutika ndi kutaya mtima, chifukwa Aisraele sadapezepo zoŵaŵa monga m'mene iyeyo ankayembekezera, ndipo zinthu sizidachitike monga m'mene mfumu idaalamulira.

Yudasi agonjetsa Lisiyasi

28Poyamba chaka china, Lisiyasi adasonkhanitsanso ankhondo oyenda pansi 60,000 ndipo okwera pa akavalo 5,000, kuti akamenyane nkhondo ndi Ayuda.

29Adapita ku Idumeya, nakamanga zithando zankhondo pafupi ndi Betizure. Yudasi adapita ndi ankhondo ake zikwi khumi kuti akakumane nawo kumeneko.

301Sam. 17.41-54; 14.1-23Poona gulu lankhondo loopsa la adaniwo, Yudasi adayamba kupemphera. Adati, “Ndinu olemekezeka, Inu Mpulumutsi wa Aisraele, Inu amene mudathyola mphamvu za chiphona chija ndi dzanja la mtumiki wanu Davide. Mudapereka gulu lankhondo la Afilisti m'manja mwa Yonatani, mwana wa Saulo, ndi m'manja mwa wonyamula zida zake.

31Tsopanonso mupereke gulu lankhondo ili m'manja mwa anthu anu Aisraele, kuti choncho anthuwo achite manyazi pamodzi ndi ankhondo ao oyenda pansi ndi okwera pa akavalo.

32Muŵachititse mantha, muŵagoole m'nkhongono, ndipo azame m'kugonja kwao.

33Muŵaphe ndi lupanga la anthu okonda Inu, ndipo onse okudziŵani alemekeze dzina lanu poimba nyimbo zothokoza.”

34Tsono adayamba kumenyana nkhondo, ndipo ankhondo 5,000 a Lisiyasi adaphedwa.

35Ataona kuti gulu lake lankhondo likugonjetsedwa, ndipo atazindikira kulimba mtima kwa Yudasi ndi anthu ake, poona kuti anthuwo ngokonzeka kukhala moyo kapena kufa monyadira, Lisiyasi adabwerera ku Antiokeya kukalemba ankhondo ena ochuluka kopambana, kuti akabwere nawo ku dziko la Yudeya.

Yudasi akonzanso Nyumba ya Mulungu

36Yudasi ndi abale ake adati, “Tsopano taŵagonjetsa adani athu. Ndiye tiyeni tipite ku Yerusalemu, kuti tikayeretse Nyumba ya Mulungu ndi kuiperekanso.”

37Motero ankhondo onse adasonkhana, nakwera ku phiri la Ziyoni.

38Kumeneko adaona Nyumba ya Mulungu itasanduka bwinja, guwa lansembe litaipitsidwa, zitseko zitapsa. Udzu unali utamera m'mabwalo ake ngati m'nkhalango kapena ku mapiri. Zipinda zogona ansembe zidaaonongeka.

39Ataona zimenezo, adang'amba zovala zao nalira kwambiri. Adadzithira phulusa ku mutu nadzigwetsa pansi chafufumimba.

40Pambuyo pake adaliza malipenga ndipo onse adalira mokweza kwa Mulungu.

41Tsono Yudasi adalamula magulu ake ena ankhondo kuti akamenyane ndi anthu okhala m'boma lankhondo, mpaka iye atatsiriza kuyeretsa Nyumba ya Mulungu.

42Ndipo adasankhula ansembe a makhalidwe abwino ndi achangu potsata Malamulo.

43Iwowo adayeretsa Nyumba ya Mulungu nakataya ku malo onyansa miyala imene akunja adaaipitsa nayo Nyumbayo.

44Pambuyo pake adafunsana zoti angachite nalo guwa la nsembe zopsereza limene akunja adaaliipitsa.

45Tsono adaganiza zopasula guwalo, kuti lingakhale chinthu choŵachititsa manyazi, popeza kuti akunja adaaliipitsa.

46Adagumula guwalo, naunjika miyala yake pa phiri la Nyumba ya Mulungu pamalo pena poyenera, mpaka atadzaoneka mneneri woŵalamula za miyalayo.

47Eks. 20.25; Deut. 27.5, 6Kenaka adatenga miyala yosasema, namangira guwa latsopano monga momwe adaanenera m'Malamulo, potsata mamangidwe a guwa lakale.

48Adakonzanso Nyumba ya Mulungu cha m'kati mwake, nayeretsa mabwalo ake.

49Adapanga ziŵiya zopatulika zatsopano, naikanso m'Nyumbamo choikaponyale, guwa lofukizirapo lubani ndi tebulo.

50Adapereka nsembe yofukiza pa guwalo, nayatsa nyale pa choikapo kuti ziziŵala m'Nyumba ya Mulungu.

51Adaikanso buledi pa tebulo, nakoloŵeka nsalu zochinga. Motero adatsiriza ntchito zonse zimene adaafuna kuzigwira.

52 1Am. 1.54 Tsono pa tsiku la 25 la mwezi wachisanu ndi chinai, mwezi wa Kisilevi, chaka cha 148, adadzuka m'mamaŵa.

53Adakapereka nsembe yopsereza pa guwa latsopano, monga momwe mudaalembedwera m'Malamulo.

54Mwezi wake ndi tsiku lake pamene akunja adaaliipitsa guwalo, ndi pomweponso pamene iwo adaliperekanso kwa Mulungu, akuimba nyimbo zothokoza ndi kuliza azeze, zitoliro ndi ziwaya za malipenga.

55Anthu onse adadzigwetsa chafufumimba, kupembedza ndi kulemekeza Mulungu amene adaŵapambanitsa.

56Adachita chikondwerero cha kupereka guwalo kwa Mulungu masiku asanu ndi atatu. Adapereka nsembe zopsereza ndi chimwemwe, ndiponso nsembe za mtendere ndi zakuthokoza.

57Pambuyo pake adakongoletsa kumaso kwa Nyumba ya Mulungu ndi tizisoti tachifumu ndi tizishango, tonseto tagolide. Kenaka adakonza zipata za Nyumba ya Mulungu ndi zipinda zogonamo ansembe, naikanso zitseko monsemo.

58Anthu onse adakondwa, pakuti manyazi amene akunja adaaŵachititsa anali atatha.

59Yudasi, abale ake ndi msonkhano wonse wa Aisraele atamvana, adalamula kuti masiku operekera guwalo kwa Mulungu azidzaŵakumbukira mwachimwemwe ndi mokondwa chaka chilichonse pa masiku asanu ndi atatu, kuyambira tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi.

60Nthaŵi yomweyo adamanga malinga aatali ndi nsanja zolimba kuzinga phiri la Ziyoni, kuti akunja angabwerenso kudzapondereza Nyumba ya Mulungu, monga adaachitira kale.

61Tsono Yudasi adaikamo gulu la ankhondo kuti azilondamo. Adamanganso malinga ankhondo ku Betizure, kuti anthu ake akhale ndi mzinda wamphamvu wopenyana ndi Idumeya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help