1Patapita ngati mwezi umodzi, Nahasi Mwamoni adanka ndi gulu lankhondo kukazinga mzinda wa Yabesi m'dziko la Giliyadi. Tsono anthu onse a mu mzinda wa Yabesi adapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe chipangano, ndipo tidzakutumikirani.”
2Koma Nahasi adaŵauza kuti, “Ndidzachita nanu chipangano pokhapokha aliyense nditamkolowola diso la ku dzanja lamanja, kuti pakutero ndichititse manyazi Aisraele onse.”
3Akuluakulu a ku Yabesi adamuyankha kuti, “Mutiyembekeze masiku asanu ndi aŵiri, kuti titumize mithenga ku dziko lonse la Aisraele. Tsono ngati sipaoneka wina wotipulumutsa, pamenepo tidzadzipereka kwa inu.”
4Pamene amithenga adafika kwao kwa Saulo ku Gibea, nauza anthu nkhaniyo, onse adayamba kulira motaya mtima.
5Nthaŵi imeneyo nkuti Saulo akuchokera ku munda, akuyenda pambuyo pa ng'ombe zantchito. Tsono adafunsa kuti, “Chaŵavuta anthu nchiyani kuti azilira?” Pamenepo adamuuza nkhani ya anthu a ku Yabesi ija.
6Saulo atamva zimenezi, pomwepo mzimu wa Mulungu udamloŵa mwamphamvu, ndipo adapsa mtima kwabasi.
7Mwa ng'ombe zija adapatulapo ziŵiri nazipha, ndipo adazidula nthulinthuli. Kenaka adatuma amithenga aja kuti akapereke nthulizo ku dziko lonse la Israele, ndi kumakanena kuti, “Umu ndimo m'mene adzaichitira ng'ombe ya aliyense amene sadzatsata Saulo ndi Samuele.”
Apo anthuwo adagwidwa ndi mantha oopa Chauta ndipo onse adanyamuka ndi mtima umodzi.
8Saulo adaŵasonkhanitsa ku Bezeki, naŵaŵerenga. Aisraele analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.
9Ndipo adauza amithenga a ku Yabesi aja kuti, “Mukaŵauze anthu akwanu kuti maŵa, dzuŵa likuwomba mtengo, adzapulumutsidwa.” Anthu a ku Yabesi atamva uthengawu, adasangalala zedi.
10Nchifukwa chake adauza Nahasi kuti, “Maŵa tidzadzipereka kwa inu, ndipo mutichite chilichonse chimene chikukomereni.”
11M'maŵa mwake, Saulo adagaŵa anthu ake m'magulu atatu. Ndipo adaloŵa pakati pa zithando zankhondo za Aamoni m'mamaŵa kusanache, napha Aamoniwo mpaka masana dzuŵa litatentha. Tsono amene adapulumuka adangoti balala, aliyense kwayekhakwayekha.
12Apo anthu adamufunsa Samuele kuti, “Ndani amene ankanena kuti, ‘Kodi Saulo nkutilamulira ife?’ Bwera nawoni anthuwo kuti tiŵaphe.”
13Koma Saulo adati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene aphedwe lero lino, pakuti lero Chauta wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele.”
14Tsono Samuele adauza anthuwo kuti, “Tiyeni tipite ku Giligala, tikatsimikizenso ufumu wa Saulo kumeneko.”
15Choncho Aisraele onse adapita ku Giligala ndipo kumeneko adalonga Sauloyo ufumu pamaso pa Chauta. Anthu adapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Chauta, ndipo Saulo pamodzi ndi Aisraele onse adasangalala zedi kumeneko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.