Mas. 115 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu mmodzi yekha woona

1Kwa ife ai, Chauta, kwa ife ai,

koma kwa dzina lanu lokha ndiye kukhale ulemerero.

Chifukwa ndinu Mulungu wa chikondi chosasinthika

ndi wokhulupirika.

2Chifukwa chiyani mitundu ina ya anthu iziti,

“Mulungu wao ali kuti?”

3Mulungu wathu ali kumwamba,

amachita chilichonse chimene afuna.

4 Mas. 135.15-18; Yere. 1.4-73; Chiv. 9.20 Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide,

opangidwa ndi manja a anthu.

5Pakamwa ali napo, koma salankhula.

Maso ali nawo, koma sapenya.

6Makutu ali nawo, koma saamva.

Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza.

7Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu.

Miyendo ali nayo, koma sayenda,

ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao.

8Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo,

chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

9Iwe Israele, khulupirira Chauta.

Chauta ndiye mthandizi wako ndi chishango chako.

10Iwe banja la Aroni khulupirira Chauta.

Chauta ndiye mthandizi wako ndi chishango chako.

11Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni.

Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu.

12Chauta watikumbukira ndipo adzatidalitsa.

Adzadalitsa anthu a Israele,

adzadalitsa banja la Aroni.

13 Chiv. 11.18; 19.5 Adzadalitsa amene amamlemekeza,

anthu wamba ndi apamwamba omwe.

14Chauta akudalitseni inu,

pamodzi ndi zidzukulu zanu zomwe.

15Akudalitseni Chauta,

amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16Kumwamba nkwa Chauta,

koma dziko lapansi adapatsa anthu.

17Akufa satamanda Chauta

otsikira ku dziko lachete satamanda Chauta.

18Koma ife tidzatamanda Chauta

kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help