1Pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yerobowamu, Abiya adaloŵa ufumu wa ku Yuda.
2Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Uriyele wa ku Gibea.
Tsono panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.
3Abiya adanyamuka kupita ku nkhondo atatenga gulu lake la ankhondo olimba mtima okwanira 400,000 osankhidwa. Yerobowamu adandanditsa ankhondo ake oti amenyane ndi Abiya, anthu okwanira 800,000, amphamvu ndi osankhidwa.
4Tsono Abiya adaima pa phiri la Zemaraimu, limene lili ku dziko lamapiri la Efuremu, ndipo adati, “Iwe Yerobowamu, pamodzi ndi Aisraele onse, imvani zimene ndikunenazi.
5Kodi simukudziŵa kuti Chauta, Mulungu wa Israele, adapereka ufumu wa Israele kwa Davide ndi kwa ana ake mpaka muyaya, pochita chipangano chosaphwanyika?
6Komabe Yerobowamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, adanyamuka naukira mbuyakeyo.
7Ndipo anthu ena achabechabe adasonkhana kwa iye nachita chipongwe Rehobowamu mwana wa Solomoni pa nthaŵi imene Rehonowamu anali wamng'ono ndi wosalimba mtima, ndipo sankatha kulimbana nawo.
8“Tsopano inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Chauta ndi kuulanda m'manja mwa ana a Davide, poti inuyo ndinu ambirimbiri. Ndipo muli nawo mafano agolide, a anaang'ombe amene Yerobowamu adakupangirani, kuti akhale milungu yanu.
9Kodi inu simudapirikitsa ansembe a Chauta, ana a Aaroni, ndiponso Alevi, ndipo mudadzisankhira ansembe anuanu, monga amachitira anthu a mitundu ina am'maikomo? Munthu aliyense amene amabwera kuti adzipereke atatenga mwanawang'ombe wamphongo kapena nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, amasanduka wansembe wa zinthu zimene sizili milungu konse.
10Koma kunena za ife, Chauta ndiye Mulungu wathu, ndipo sitidamsiye ai. Tili nawo ansembe, ana a Aaroni, otumikira Chauta, tilinso ndi Alevi amene amatumikira ansembewo.
11Iwowo amapereka kwa Chauta nsembe zopsereza m'maŵa mulimonse ndi madzulo aliwonse. Amafukiza lubani wonunkhira bwino, amaikanso buledi wopereka pa tebulo la golide weniweni, namasamala zoikapo nyale zagolide, kuti nyale zake ziziyaka madzulo aliwonse. Ife timasunga zimene Chauta Mulungu wathu amatilamula, koma inuyo mudamsiya.
12Onani, Mulungu ali nafe, akutitsogolera, ansembe ake atatenga malipenga ao ankhondo otiitanira ku nkhondo yokamenyana ndi inu. Inu ana a Israele, musati mulimbane ndi Chauta, Mulungu wa makolo anu, chifukwa simungathe kupambana.”
13Yerobowamu anali atatumiza anthu obisalira, kuti alimbane nawo moŵadzera kumbuyo. Motero magulu ankhondowo anali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, ndipo obisalirawo anali kumbuyo kwao.
14Anthu a ku Yuda aja poyang'ana, adangoona kuli nkhondo kutsogolo kwao ndi kumbuyo komwe. Tsono adafuula kwa Chauta, ndipo ansembe adayamba kuliza malipenga.
15Apo anthu a ku Yuda adafuula, kufuula kwake kwankhondo. Ndipo anthu a ku Yudawo atafuula, Mulungu adagonjetsa Yerobowamu pamodzi ndi anthu a ku Israele onse, pamaso pa Abiya ndi pa anthu a ku Yuda.
16Aisraele adathaŵa Ayuda, ndipo Mulungu adapereka Aisraelewo kwa Ayuda.
17Abiya pamodzi ndi anthu ake adapha Aisraelewo, kupha kwake kwakukulu. Adaphedwa Aisraele okwanira 500,000, anthu ndithu osankhidwa.
18Motero Aisraele adagonjetsedwa nthaŵi imeneyo, ndipo Ayuda adapambana chifukwa chakuti adakhulupirira Chauta, Mulungu wa makolo ao.
19Tsono Abiya uja adapirikitsa Yerobowamu, namlanda mizinda iyi: Betele ndi midzi yake, Yasana ndi midzi yake, ndiponso Efuroni ndi midzi yake.
20Yerobowamu sadapezenso mphamvu nthaŵi ya Abiya. Ndipo Chauta adamkantha Yerobowamu, naafa.
21Koma Abiya mphamvu zake zidakula. Ndipo adakwatira akazi khumi ndi anai, nabala ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16.
22Ntchito zonse za Abiya, makhalidwe ake ndi zimene ankalankhula zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Ido.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.