1Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu.
2 Imeneyi ndi mitundu ya anthu okhala ku mphepo zonse zinai. Satana adzaŵasonkhanitsa pamodzi kuti achite nkhondo. Kuchuluka kwao ndi ngati mchenga wakunyanja.
9Adayenda pa dziko lonse lapansi, nazinga misasa ya anthu a Mulungu, ndi mzinda umene Mulungu amaukonda. Koma moto udatsika kuchokera Kumwamba nkudzaŵaononga.
10Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.
Za chiweruzo chotsiriza11 Dan. 7.9, 10 Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse.
122Es. 6.20Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo.
13Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake.
14Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.
15Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.