Chiv. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano

1 Yes. 65.17; 66.22; 2Pet. 3.13 Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.

22Es. 13.36; Yes. 52.1; Chiv. 3.12; Yes. 61.10Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.

3Ezek. 37.27; Lev. 26.11, 12Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao.

4Yes. 25.8; Yes. 35.10; 65.19Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”

5Pamenepo wokhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.” Adanenanso kuti, “Lemba zimenezi, pakuti mau ameneŵa ndi oona ndi oyenera kuŵakhulupirira.”

6Yes. 55.1Adandiwuzanso kuti, “Kwatha! Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti, Woyamba ndi Wotsiriza ndine. Aliyense womva ludzu, ndidzampatsa mwaulere madzi a pa kasupe wa madzi opatsa moyo.

72Sam. 7.14; Mas. 89.26, 27Aliyense amene adzapambane, adzalandira zimenezi, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wake, iye adzakhala mwana wanga.

8Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Za Yerusalemu watsopano

9Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri yodzaza ndi miliri isanu ndi iŵiri yotsiriza ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno, ndikakuwonetse mkwati, mkazi wa Mwanawankhosa uja.”

10Ezek. 40.2; 2Es. 10.27Pamenepo mngelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu.

11Unkaŵala ndi ulemerero wa Mulungu. Kuŵala kwake kunali ngati kuŵala kwa mwala wamtengowapatali, ngati mwala wambee, wonyezimira ngati galasi.

12Ezek. 48.30-35Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.

13Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu.

14Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi aŵiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa uja.

15 Ezek. 40.3 Mngelo amene ankalankhula naneyo anali ndi ndodo yoyesera yagolide, yoti ayesere mzinda uja, zipata zake ndi linga lake.

16Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana.

17Kenaka adayesa linga la mzindawo, napeza kuti msinkhu wake unali mamita 65. Mngeloyo ankayesa ndi muyeso womwe anthu amagwiritsa ntchito.

18Yes. 54.11, 12

Tob. 13.16, 17Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi.

19Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira;

20achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira.

21Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi.

22Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja.

23Yes. 60.19, 20Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja.

24Yes. 60.3Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo.

25Yes. 60.11Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku.

26Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao.

27Yes. 52.1; Ezek. 44.9Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help