1 Yes. 52.1; 61.3, 10; Chiv. 21.2 Iwe Yerusalemu, vula chovala chako chamaliro
ndi chachisoni.
Uvale mpaka muyaya zovala za ulemerero wa Mulungu.
2Funda mwinjiro wachilungamo
wochokera kwa Mulungu.
Vala chisoti cha ulemerero wa Mulungu wamuyaya.
3Chifukwa Mulungu akufuna kuŵonetsa ulemerero wako
kwa onse okhala pansi pa thambo lakumwamba.
4Mulungu adzakutcha dzina
limene mpaka muyaya lidzakhala
“Mtendere wa chilungamo,”
ndipo “Ulemerero wa chipembedzo.”
5Dzuka, iwe Yerusalemu,
imirira pamtundapo,
uyang'ane kuvuma.
Ona ana ako amene Woyera uja waŵasonkhanitsa
kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe.
Akukondwa pakuti Mulungu waŵakumbukira.
6Adakusiya akuyenda pansi,
adani ao ataŵatenga.
Koma Mulungu adzaŵabwezanso kwa iwe,
ataŵanyamula mwaulemerero
ngati ana a ku nyumba ya mfumu.
7Pajatu Mulungu adalamula
kuti mapiri aatali ndi zitunda zosatha azichepetse,
ndiponso kuti zigwa azifotsere
kuti mbali zonse zilingane.
Motero Aisraele adzayenda mwamtendere
mu ulemerero wa Mulungu.
8Potsata lamulo la Mulungu
nkhalango ndi mitengo yonse ya fungo labwino
zidzaŵakonzera mthunzi Aisraele.
9Zoonadi Mulungu adzatsogolera Aisraele mwachimwemwe
ndi kuŵala kwa ulemerero wake,
ndiponso ndi chifundo ndi chilungamo chake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.