Mas. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo ya Davide atagonjetsa adani(2 Sam. 22.1-51)Kwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide, mtumiki wa Chauta.Nyimbo imeneyi adaimbira Chauta, atampulumutsa kwa adani ake onse, makamaka kwa Saulo. Adati:

1Ndimakukondani Chauta,

Inu mphamvu zanga.

2Chauta ndiye thanthwe langa,

linga langa ndi mpulumutsi wanga.

Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa

limene ndimathaŵirako.

Ndiye chishango changa,

ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga,

ndiye linga langa.

3Ndimaitana Chauta,

amene ayenera kumtamanda,

ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.

4Nthambo za imfa zidandizungulira,

mitsinje yothamanga yoononga idandisefukira.

5Nthambo zakumanda zidandizeŵeza,

misampha ya imfa idandikola.

6Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga.

Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.

Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa,

kulira kwanga kofuna chithandizo

kudamveka kwa iye.

7Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera

ndi kuchita chivomezi.

Maziko a mapiri nawonso adanjenjemera ndi kugwedezeka,

chifukwa Iye adaakalipa.

8M'mphuno mwake munkafuka utsi,

m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga,

makala amoto anali laŵilaŵi

kuchokera m'kamwa momwemo.

9Adang'amba thambo natsika pansi,

mdima wabii unali ku mapazi ake.

10Adakwera pa mkerubi nauluka.

Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo.

11Mdima adausandutsa chofunda chake,

mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake.

12M'kuŵala kumene kunali pamaso pake,

munkafumira matalala ndi makala amoto,

amene adabzola mitambo yophimba ija.

13Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu,

Wopambanazonse liwu lake lidamveka

m'kati mwa matalala ndi makala amoto.

14Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,

adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa.

15Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera,

maziko a dziko lapansi adakhala poyera,

pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa,

pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu.

16Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira,

ndi kundivuula m'madzi ozama.

17Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu,

kwa onse amene ankadana nane,

pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine.

18Adaniwo adandithira nkhondo

pamene ndinali m'mavuto,

koma Chauta adandichirikiza.

19Adakandifikitsa ku malo amtendere,

adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane.

20Chauta adandipatsa mphotho

molingana ndi ntchito zanga zabwino,

adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.

21Ine ndidatsata njira za Chauta,

sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga.

22Ndidamvera malangizo ake onse,

ndipo malamulo ake sindidaŵataye.

23Ndinalibe mlandu pamaso pake,

ndinkalewa zoipa m'moyo mwanga.

24Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho

molingana ndi ntchito zanga zabwino,

monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu.

25Kwa anthu okhulupirika,

Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika.

Kwa anthu aungwiro,

mumadziwonetsa abwino kotheratu.

26Kwa anthu oyera mtima

mumadziwonetsa okoma mtima,

koma kwa anthu oipa mtima,

mumawonetsa kunyansidwa nawo.

27Paja anthu odzichepetsa,

Inu mumaŵapulumutsa,

koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa.

28Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga.

Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima.

29Ndi chithandizo chanu

ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo.

Ndi chithangato cha Mulungu,

ndingathe kupambana.

30Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro,

mau ake sapita pachabe,

Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.

31Palibe mulungu wina koma Chauta yekha.

Palibe thanthwe lina lothaŵirapo

koma Mulungu wathu yekha.

32Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu,

wandichotsera zoopsa m'njira zanga.

33 Hab. 3.19 Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala,

ndipo amandisunga bwino m'mapiri.

34Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo,

kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.

35Inu mwanditchinjiriza

ndi chishango chanu chachipulumutso.

Dzanja lanu lamanja landichirikiza,

mwandikweza ndi chithandizo chanu.

36Mudandikuzira njira yanga kuti ndiyendemo bwino,

choncho mapazi anga sadaterereke.

37Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza,

sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa.

38Ndimaŵakantha koopsa

kotero kuti sangathenso kudzuka,

ndidaŵapondereza ndi mapazi anga.

39Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo,

ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.

40Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe,

amene ankadana nane ndidaŵaononga.

41Adakuwa kuti ena aŵathandize,

koma panalibe woŵapulumutsa.

Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe.

42Ndidaŵaperapera ngati fumbi louluka ndi mphepo.

Ndimaŵapondereza ngati matope amumseu.

43Inu mudandipulumutsa kwa anthu olimbana nane,

Inu mudandisandutsa mfumu ya mitundu yonse.

Choncho anthu osaŵadziŵa ankanditumikira.

44Atangomva za ine adayamba kundimvera,

anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba.

45Anthu a mitundu ina adataya mtima,

adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje.

46Chauta ndi wamoyo.

Litamandike thanthwe langa,

alemekezeke Mulungu wondipulumutsa,

47Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire,

adagonjetsa anthu a mitundu ina,

kuti akhale mu ulamuliro wanga.

48Ndiye amene adandipulumutsa kwa adani anga.

Zoonadi Inu mudandikweza pamwamba pa ondiwukira,

mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.

49 Aro. 15.9 Chifukwa cha zimenezi ndidzakutamandani Inu Chauta,

pakati pa mitundu ya anthu,

ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.

50Mulungu amathandiza mfumu yake,

kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi.

Amaonetsa chikondi chake chosasinthika

kwa wodzozedwa wake,

ndiye kuti kwa Davide

ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help