1Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,
tinali ngati anthu amene akulota.
2Pamenepo tidasekera kwambiri,
ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.
Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti,
“Chauta waŵachitira zazikulu.”
3Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,
ndipo tasangalala.
4Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,
tikhale ngati mitsinje yam'chipululu.
5Anthu amene amafesa akulira,
adzakolola akufuula ndi chimwemwe.
6Munthu amene amapita akulira,
atatenga mbeu zokafesa,
adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe,
atatenga mitolo yake yambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.