Mas. 79 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha kuti mtundu wonse upulumukeSalmo la Asafu.

1 2Maf. 25.8-10; 2Mbi. 36.17-19; Yer. 52.12-14 Inu Mulungu, anthu akunja aloŵerera

m'dziko la anthu anu,

aipitsa Nyumba yanu yoyera.

Asandutsa Yerusalemu bwinja.

2Ataya mitembo ya atumiki anu

kwa mbalame zamumlengalenga,

kuti ikhale chakudya chake,

ataya matupi a anthu anu oyera mtima

kwa zilombo zakuthengo.

3Akhetsa magazi ao ngati madzi,

ponse pozungulira Yerusalemu,

ndipo palibe woti nkuika maliro ao.

4Ife tasanduka chinthu chonyozeka kwa anzathu,

anthu a mitundu ina amatinyodola ndi kutiseka.

5Mpaka liti, Inu Chauta?

Kodi mudzakhalabe wokwiya mpaka muyaya?

Kodi nsanje yanu idzayakabe ngati moto?

6Gwetsani ukali wanu pa mitundu ya anthu osakudziŵani,

ndiponso pa maufumu osatama dzina lanu mopemba.

7Pakuti ameza anthu a Yakobe,

ndipo dziko lao alisandutsa bwinja.

8Musatilange ife chifukwa cha machimo a makolo athu.

Mutichitire chifundo msanga,

chifukwa tatsitsidwa kwambiri.

9Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,

kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero.

Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu,

kuti dzina lanu lilemekezeke.

10Chifukwa chiyani anthu akunja akuti,

“Kodi Mulungu wao ali kuti?”

Mulole kuti tiwone Inu mukulipsira mitundu ina ya anthu,

chifukwa chokhetsa magazi a atumiki anu.

11Mumve kubuula kwa anthu am'ndende,

muŵasunge ndi mphamvu zanu zazikulu

anthu oyenera kuphedwa.

12Inu Ambuye, kunyoza kuja

kumene anthu a mitundu ina adakunyozani,

muŵabwezere kasanunkaŵiri.

13Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pa busa lanu,

tidzakuthokozani mpaka muyaya,

tidzakutamandani m'mibadwo yonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help