1 Sam. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide adzozedwa kuti akhale mfumu.

1Chauta adauza Samuele kuti, “Kodi udzakhala ukumlirabe Saulo mpaka liti, poti ndamkana kuti asakhalenso mfumu yolamulira Aisraele? Dzaza mafuta m'nsupa yakoyi. Upite kwa Yese wa ku Betelehemu, poti ndadzipezera mfumu pakati pa ana ake aamuna.”

2Samuele adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndingathe bwanji kupitako? Saulo akamva zimenezi, adzandipha.” Chauta adati, “Utenge ng'ombe yaikazi popita, ndipo ukanene kuti, ‘Ndadzapereka nsembe kwa Chauta.’

3Uitane Yese kunsembeko, tsono Ine ndikakulangiza zoti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakutchulire.”

4Samuele adachitadi zimene Chauta adalamula, nakafika ku Betelehemu. Atsogoleri amumzindamo adadzamchingamira ali njenjenje, ndipo adamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino?”

5Samuele adayankha kuti, “Inde, nkwabwino. Ndadzapereka nsembe kwa Chauta. Mudzipatule, ndipo mupite nane kukapereka nsembe.” Pamenepo Samuele adapatula Yese ndi ana ake aamuna, ndipo adaŵaitana kuti akapereke nao nsembe.

6Onsewo atafika, Samuele adayang'ana Eliyabu namaganiza kuti, “Ndithudi amene Chauta adamsankha ndi uyu ali pamaso pakeyu.”

7Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”

8Tsono Yese adaitana Abinadabu namtumiza kwa Samuele. Ndipo Samuele adati, “Ameneyunso Chauta sadamsankhe.”

9Pamenepo Yese adaitana Sama kuti apite kwa Samuele. Koma Samuele adati, “Ameneyunso Chauta sadamsankhe.”

10Choncho Yese adatumiza ana ake aamuna asanu ndi aŵiri kuti apite kwa Samuele. Koma Samueleyo adati, “Chauta sadaŵasankhe ameneŵa.”

11Tsono adafunsa Yese kuti, “Kodi ana ako aamuna ndi okhaŵa?” Yeseyo adati, “Alipo wina wamng'ono, mzime, amene watsala, koma iyeyo akuŵeta nkhosa.” Apo Samuele adauza Yese kuti, “Mtumireni munthu, akamtenge, pakuti sitipereka nsembe mpaka iyeyo atabwera pano”

12Choncho adatuma munthu kukamtenga, ndipo adabwera naye. Anali wofiirira ndi wa maonekedwe okongola ochititsa kaso. Pamenepo Chauta adati, “Ndi ameneyu, mdzoze.”

13Samuele adatenga nsupa ya mafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamloŵa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama.

Davide atumikira Saulo.

14Nthaŵi imeneyo mzimu wa Chauta udaamchokera Saulo ndipo mzimu wina woipa, wotumidwa ndi Chauta, udayamba kumzunza.

15Atumiki ake adamuuza kuti, “Onani, tsopano mzimu woipa, wotumidwa ndi Mulungu, ukukuzunzani.

16Ndiye inu mbuyathu, tilamuleni antchito anufe pano kuti tifunefune munthu waluso poimba zeze. Mzimu woipawu ukakufikirani, munthuyo azidzaimba zeze, ndipo mudzapeza bwino.”

17Pamenepo Saulo adaŵauza kuti, “Chabwino mundifunire munthu wodziŵa bwino kuimba kwake, ndipo mubwere naye kuno.”

18Mmodzi mwa antchitowo adati, “Ndaona mwana wamwamuna wa Yese wa ku Betelehemu amene ali wokhoza zeze, munthu wolimba mtima, ngwazi pankhondo, wochenjera polankhula, munthu wokongola. Ndipo Chauta ali naye.”

19Choncho Saulo adatuma amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Tumizire Davide mwana wako, uja amaŵeta nkhosayu.”

20Yese adatenga bulu namsenzetsa buledi, thumba lachikopa la vinyo ndi mwanawambuzi. Zonsezo adapatsa Davide mwana wake, kuti akazipereke kwa Saulo.

21Motero Davide adafika kwa Saulo, nayamba ntchito yake yomtumikira. Saulo adamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake zankhondo.

22Kenaka Saulo adatumiza mau kwa Yese kuti, “Davide akhale womanditumikira, pakuti ndamkonda kwambiri.”

23Tsono nthaŵi zonse mzimu woipa uja ukamfikira Saulo, Davide ankatenga zeze namamuimba. Motero Saulo ankapeza bwino, ndipo mzimu woipawo unkamsiya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help