Mas. 92 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Salmo lotamandiraNyimbo ya pa Sabata.

1Nkwabwino kuthokoza Chauta,

kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu,

Inu Wopambanazonse.

2Nkwabwino m'maŵa

kulalika za chikondi chanu chosasinthika,

ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,

3poimba nyimbo zokoma ndi gitara,

zeze ndi pangwe.

4Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu.

Motero ndikufuula ndi chimwemwe

chifukwa cha zimene Inu mwachita.

5Ntchito zanu si kukula kwake, Inu Chauta!

Maganizo anu si kuzama kwake!

6 Lun. 13.1 Munthu wopanda nzeru sangadziŵe,

munthu wopusa sangamvetse zimenezi, zakuti,

7ngakhale anthu oipa aziphuka ngati udzu,

ndipo anthu ochimwa zinthu ziziŵayendera bwino,

kwao nkuwonongeka kwamuyaya.

8Inu nokha Chauta,

ndinu Wopambanazonse mpaka muyaya.

9Ndithudi adani anu, Inu Chauta,

adani anu adzaonongeka,

onse ochita zoipa adzamwazikana.

10Koma ine mwandilimbitsa ngati njati.

Mwandidzoza ndi mafuta atsopano.

11Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga,

makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira.

12Anthu okondweretsa Mulungu

zinthu zimaŵayendera bwino

ngati mitengo ya mgwalangwa,

amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.

13Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta,

yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.

14Mitengoyi imabalabe zipatso

ngakhale itakalamba,

nthaŵi zonse imakhala ndi madzi

ndipo imabiriŵira,

15imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama.

Iye ndiye thanthwe langa

mwa Iye mulibe chokhota.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help