Ahe. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau a Mulungu kudzera mwa Mwana wake

1Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri.

2Lun. 7.22 Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake.

3Lun. 7.25, 26; 8.1 Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.

Za ukulu wake wa Mwana wa Mulungu

4Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo.

5Mas. 2.7; 2Sam. 7.14; 1Mbi. 17.13 Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti,

“Iwe ndiwe mwana wanga,

Ine lero ndakubala.”

Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti,

“Ine ndidzakhala bambo wake,

iye adzakhala mwana wanga.”

6 Deut. 32.43 Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati,

“Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”

7 Mas. 104.4 Ndipo za angelo Mulungu adati,

“Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo,

atumiki ake amaŵasandutsa malaŵi a moto.”

8 Mas. 45.6, 7 Koma za Mwana wake adati,

“Inu Mulungu,

mpando wanu wachifumu udzakhala mpaka muyaya,

chilungamo ndicho chili ngati ndodo yachifumu

mu ulamuliro wanu.

9Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama.

Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani

nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe,

kupambana anzanu ena onse.”

10 Mas. 102.25-27 Adatinso,

“Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi

pachiyambi pomwe,

zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu.

11Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire.

Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala.

12Mudzazipindapinda ngati mwinjiro,

ndipo zidzasinthika ngati chovala,

koma Inu ndinu osasinthika,

zaka zanu sizidzatha konse.”

13 Mas. 110.1 Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti,

“Khala ku dzanja langa lamanja

mpaka ndisandutse adani ako

kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.”

14 Tob. 12.14, 15 Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help