Bar. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mphu. 24.23 Nzeru ndiye buku la Malamulo a Mulungu.

Malamulo ake odzakhala mpaka muyaya.

Onse ozigwiritsa nzeruzo, amakhala ndi moyo,

koma olekana nazo amafa.

2Bwerera Yakobe, udzalandire nzeru,

yenda molondola kuŵala kwa kuyera kwake.

3Ulemerero wako usapatse munthu wina,

madalitso ako usaŵapereke kwa anthu achilendo.

4Inu Aisraele, ifetu ndife odala,

chifukwa timadziŵa zokomera Mulungu.

Yerusalemu alimbikitsa chikhulupiriro cha ana ake

5Limbani mtima, anthu anga,

inu amene mumamveketsa dzina la Israele.

6Adakugulitsani kwa anthu akunja,

koma osati kuti muwonongekeretu.

Mudakwiyitsa Mulungu,

nkuwona adakuperekani kwa adani anu.

7Mudamputadi Mlengi wanu

popereka nsembe ku mafano,

m'malo mozipereka kwa Mulungu.

8Mudaiŵala Mulungu wamuyaya

amene adakulerani.

Mudamvetsa chisoni Yerusalemu

amene anali ngati mai wanu.

9Iye adaona ukali wa Mulungu ukukugwerani,

ndipo adati,

“Mvetserani, inu anthu okhala pafupi ndi Ziyoni,

Mulungu wanditumizira mavuto aakulu.

10“Ndidaonerera ana anga aamuna ndi aakazi

akutengedwa kupita nawo kuukapolo

kumene Mulungu wamuyaya adaŵatumiza.

11Ndinkaŵalera ndi chimwemwe,

koma poŵaona akutengedwa ukapolo,

ndidamva chisoni ndi kulira misozi.

12Ndiye wina aliyense asakondwerere mavuto angaŵa,

pamene tsopano ndili wamasiye,

ndipo ana anga ambiri adandisiya.

Ndidakhala choncho ndekhandekha

chifukwa cha machimo a ana angawo,

popeza kuti iwowo adasiya malamulo a Mulungu.

13Sadalabadeko nkomwe za malamulo ake,

sadatsate konse njira za malamulo ake,

sadalole kuti Mulungu aŵaongolere

m'njira ya chilungamo.

14“Tsono bwerani kuno,

inu anthu okhala pafupi ndi Ziyoni!

Kumbukirani ukapolo wa ana anga aamuna ndi aakazi

ku dziko lachilendo

kumene Mulungu wamuyaya adaŵatumizako moŵalanga.

15Paja Mulungu adaŵadzetsera

mtundu wa anthu akutali,

kuti udzaŵathire nkhondo,

mtundu wopanda manyazi,

wolankhula chilankhulo chosadziŵika,

mtundu wosalemekeza anthu okalamba,

mtundu wosamvera chifundo ndi ana omwe.

16Anthu a mtundu umenewu

adatenga ana aamuna okondedwa a mai wamasiye,

adalanda ana aakazi a mai wotsala yekha,

kumusiya nalira.

17“Nanga ine ndingakuthandizeni bwanji?

18Pajatu amene adakugwetserani mavuto ameneŵa

ndi iyeyo amene angakupulumutseni kwa adani anu.

19 2Es. 2.2 Pitani ana anga, inde pitani!

Ine ndatsala ndekha.

20Ndavula mkanjo wa masiku amtendere,

ndavala chiguduli chamaliro.

Ndidzalira kwa Mulungu wanga wamuyaya

pa moyo wanga wonse.

21“Limbani mtima, ana anga,

pempherani kwa Mulungu.

Iye adzakupulumutsani ku mavuto

ndiponso kwa adani anu.

22Inetu ndikukhulupirira

kuti Mulungu wamuyaya adzakupulumutsani.

Woyera uja wandisangalatsa

chifukwa cha chifundo

chimene chidzakufikireni posachedwapa

kuchokera kwa Mpulumutsi wanu wamuyaya.

23Ndidakuwonererani mukupita kutali

muli ndi chisoni mu mtima ndi misozi m'maso.

Koma Mulungu adzakubwezaninso kwa ine

muli ndi chimwemwe ndi chisangalalo,

kuti mukhale nane mpaka muyaya.

24Anthu okhala pafupi ndi Ziyoni amene

adakuwonani mukutengedwa ukapolo,

posachedwa adzaona Mulungu akukupulumutsani.

Chipulumutsocho chidzakufikirani

ndi ulemerero waukulu

ndiponso ndi ukulu wodabwitsa wa Mulungu wamuyaya.

25Ana anga, pirirani mosaŵinya

mkwiyo wa Mulungu umene udakugwerani.

Adani anu adakusautsani,

koma posachedwa mudzaŵaona akuwonongeka,

mudzaŵaponda pa khosi ndi mapazi anu.

26Ana anga okondedwa adayenda m'njira zokhakhala,

ndipo adaŵatenga ngati gulu la zoŵeta

zimene mdani wazifunkha.

27“Limbani mtima, ana anga,

pempherani kwa Mulungu,

chifukwa amene adakulangani chotereyo,

yemweyonso adzakukumbukirani.

28Monga mwa kufuna kwanu mudasiyana ndi Mulungu,

momwemonso mutembenukire kwa Iye,

mumufunefune ndi mtima wanu wonse.

29Pakuti monga momwe Iye adakugwetserani m'mavuto,

momwemonso adzakupulumutsani,

ndipo mudzakhala osangalala mpaka muyaya.”

Asangalatsa Yerusalemu

30Limba mtima, iwe Yerusalemu.

Amene adakutcha dzina uja,

yemweyonso adzakusangalatsa.

31Anthu amene adakuchita zoipa,

nkukondwerera kuwonongeka kwako,

adzapeza mavuto.

32Kumizinda kumene ana ako adakazunzikirako ukapolo,

kudzaoneka mavuto.

Mavutonso adzagwera mzinda

umene udalandira ana ako ngati akaidi.

33Pakuti monga momwe mzindawo udakondwerera

kugwa kwako,

nkusangalala chifukwa cha kuwonongeka kwako,

momwemonso mzindawo udzavutika

pamene uwo womwewo udzapasuka.

34Ndidzauchotsera chimwemwe

chonyadira kuchuluka kwa anthu ake,

chikondwerero chake chidzasanduka maliro.

35Moto wochokera kwa Mulungu wamuyaya

udzatentha mzindawo pa masiku ambiri,

ndipo kumeneko kudzakhala ademoni

pa nthaŵi yaitali.

36Yang'ana kuvuma, iwe Yerusalemu,

ona chimwemwe chimene Mulungu akukutumizira.

37Ona alikudza ana ako,

amene udaŵaonerera akupita ku dziko lachilendo.

Alikudzadi,

Woyera uja ataŵasonkhanitsa

kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe,

akukondwerera ulemerero wa Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help