1 Zef. 2.12 Tsoka kwa anthu okhala ku dziko la
patsidya pa mitsinje ya Etiopiya!
Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko.
2Kuchokera ku dzikolo amatuma akazembe
pa mtsinje wa Nailo m'mabwato agumbwa
omangoyandama pa madzi.
Tsono pitani inu amithenga aliŵiro
kwa mtundu wa anthu ataliatali
ndi a khungu losalala,
oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe,
mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina,
anthu amene dziko lao nlodukanadukana ndi mitsinje.
3Inu nonse anthu a pa dziko lapansi,
inu amene mumakhala pansi pano,
pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri,
muyang'ane!
Lipenga likamalira, mumve!
4Pakuti Chauta adandiwuza kuti,
“Kumene ndili Ineko,
ndidzangoyang'ana pansi mwakachetechete,
monga m'mene dzuŵa limaŵalira nthaŵi yotentha,
monganso m'mene amagwera mame usiku
pa nthaŵi yakholola.”
5Anthu asanayambe kukolola, maluŵa
atayoyoka ndipo mphesa zitayamba kupsa,
Iye adzadula mphukira ndi chigwandali,
ndipo adzasadza nthambi zotambalala.
6Mitembo ya ankhondowo adzasiyira
mbalame zam'mapiri zodya nyama,
ndiponso zilombo zakuthengo.
Mbalame zidzaidya pa nthaŵi ya chilimwe,
ndipo zilombo zakuthengo
zidzaidya pa nthaŵi ya chisanu.
7Pa nthaŵi imeneyo
anthu adzabwera ndi zopereka
kwa Chauta Wamphamvuzonse.
Anthu ake adzakhala aatali ndi a khungu losalala,
oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe,
mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina,
anthu amene dziko lao ndi lodukanadukana ndi mitsinje.
Zoperekazo adzabwera nazo ku phiri la Ziyoni
kumene anthu amapembedza Chauta Wamphamvuzonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.