1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, uŵaphere mwambi Aisraele ndi kuŵauza fanizo.
3Unene kuti Ambuye Chauta akuti, Panali chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko akuluakulu, ndi nthenga zitalizitali za mathothomathotho. Chidadza ku Lebanoni. Chidagwira nthambi yapamwamba pa mtengo wa mkungudza,
4nkubudula nsonga yeniyeni ya nthambiyo. Chidapita nayo ku dziko lamalonda, nkukaiika mu mzinda wa anthu amalonda.
5Kenaka chidatenga mbeu ya m'dzikomo nkukaibzala pa malo achonde, pamene panali madzi ambiri pafupi. Chidaibzala monga momwe amabzalira mtengo wa msondodzi.
6Tsono idaphuka nisanduka mtengo wamphesa wotambalala cham'munsi. Nthambi zake zidaloza kumwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake idazamira pansi. Choncho mtengo wamphesawo udasanduka wanthambi ndi wa masamba ambiri.
7“Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu cha mapiko akuluakulu ndi cha nthenga zambiri. Mtengo wamphesa uja udapinda mizu yake kulozetsa kwa chiwombankhangacho. Ndipo udayang'anitsa nthambi zake kwa chimbalamecho, kuti mwina nkuzithirira madzi oposa amene anali m'mundamo.
8Koma mtengowo adaauwoka kale m'nthaka yachonde m'mene munali madzi ambiri, kuti uphuke nthambi ndi kubereka mphesa, ndi kukhala wokongola.
9“Ukanene kuti, Ambuye Chauta akuti, Kodi mtengo wamphesa umenewu udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzauzula mizu ndi kubudula nthambi zake, kotero kuti masamba ake anthete adzafota? Nkosalira munthu wamphamvu kapena anthu ochuluka kuti auzuletu ai.
10Tsono ngakhale atauwoka pena, kodi udzakula bwino? Kodi sudzafota kotheratu ikadzaomba mphepo yakuvuma, kufotera pomwe auwokerapo?”
Amasulira fanizolo11Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
122Maf. 24.15-20; 2Mbi. 36.10-13 “Uŵafunse anthu aupanduŵa kuti, ‘Kodi mukulidziŵa tanthauzo lake la zimenezi?’ Uŵauze kuti mfumu ya ku Babiloni idaapita ku Yerusalemu, nikatengako mfumu ndi akalonga ake kupita nawo ku Babiloni.
13Idatenga mwana wina wa mfumu nkuchita naye chipangano, ndipo idamlumbiritsa kuti akhale womvera. Idachotsa akulu onse am'dzikomo,
14kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzatchukenso, koma kuti ukhalepobe pakungosunga chipangano chimene udachita.
15Koma mfumuyo idapandukira mfumu ya ku Babiloni, nitumiza akazembe ku Ejipito kukapempha akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Kodi mfumu yoteroyo ingapambane? Kodi ingathe kupulumuka ngati ichita zotero? Kodi ingathe kuphwanya chipangano, kenaka nkupulumuka?”
16“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikulumbira pali Ine ndemwe wamoyo, kuti mfumuyo idzafera ku Babiloni, dziko lomwe la mfumu imene idamulonga ufumuyo. Idapeputsa lumbiro lake, nkuphwanya chipangano chimene idachita ndi mfumu inayo. Motero idzafera ku Babiloni.
17Farao pamodzi ndi gulu lake lankhondo adzalephera kuithandiza mfumuyo pamene ankhondo a ku Babiloni adzazinga mzinda wake ndi mitumbira yankhondo ndi nsanja zankhondo, kuti aononge anthu ambiri.
18Mfumu ya ku Yuda idanyoza lumbiro lake pakuphwanya chipangano. Idaalonjeza, komabe sidatsate malonjezowo. Choncho sidzapulumuka.
19“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, iyeyo wapeputsa lumbiro lake limene adalumbira kwa Ine, ndipo waphwanya chipangano chimene ndidapangana naye. Motero ndidzamlanga chifukwa cha zoipa zake.
20Ndidzamtchera ukonde, ndipo ndidzamkola mu msampha wanga. Ndidzamtengera ku Babiloni, ndipo ndidzamlangira komweko, chifukwa choti sadakhulupirike kwa Ine.
21Asilikali ake onse amphamvu adzaphedwa ku nkhondo, ndipo opulumuka adzathaŵira ku mbali zonse. Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta amene ndanena zimenezi.”
Za madalitso akutsogolo22Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Ine ndemwe ndidzatenga kanthambi ka ku nsonga yapamwamba ya mtengo wa mkungudza, ndipo ndidzakabzala. Pa tinthambi tapamwamba ndidzathyolako kena kanthete ndipo ndidzakabzala pa phiri lalitali kwambiri.
23Ndidzakabzaladi pa phiri lalitali la ku Israele. Kadzaphuka ndi kubala zipatso zake. Motero kadzasanduka mkungudza wokoma. Mbalame za mitundu yonse zidzakhala mu mthunzi wa mtengowo.
24Mitengo yonse yam'dzikomo idzadziŵa kuti ndine Chautane amene ndimafupikitsa mitengo yaitali, ndiponso kutalikitsa mitengo yaifupi. Ndimaumitsa mitengo yobiriŵira, ndi kubiriŵiritsa mitengo youma. Ine Chauta ndanena zimenezi, ndipo ndidzazichitadi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.