1
Ndani angaime m'malo ake oyera?
4 Mt. 5.8 Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake,
ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake.
Ndi amene salingalira zonama,
ndipo salumbira monyenga.
5Adzalandira madalitso kwa Chauta,
ndipo Mulungu Mpulumutsi wake
adzagamula kuti alibe mlandu.
6Anthu otere ndiwo amene amafunitsitsa Chauta,
ndiwo amene amabwera kudzapembedza Mulungu wa Yakobe.
7Kankhani zipata za mzinda,
tsekulani zitseko zakalekalezo,
kuti Mfumu yaulemerero iloŵe.
8Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu,
Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
9Kankhani zipata za mzinda,
tsekulani zitseko zakalekalezo,
kuti Mfumu yaulemerero iloŵe.
10Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.