1Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.”
2Yesu adati, “Pamene mukupemphera muziti,
“ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe.
Ufumu wanu udze.
3Mutipatse ife tsiku lililonse
chakudya chathu chamasikuwonse.
4Mutikhululukire ife machimo athu,
pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ”
5Adaŵauzanso kuti, “Tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, ‘Iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu?
6Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse.’
7Koma wam'nyumbayo nkuyankha kuti, ‘Usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’
8Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusoŵa.
9“Motero ndikukuuzani kuti, Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
10Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
11Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?
12Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira?
13Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Za Yesu ndi Belezebulu(Mt. 12.22-30; Mk. 3.20-27)14Tsiku lina Yesu ankatulutsa mzimu woipa woletsa munthu kulankhula. Mzimuwo utatuluka, munthu amene anali wosalankhulayo adayamba kulankhula, mwakuti anthu ambirimbiri amene anali pomwepo adazizwa kwabasi.
15
17Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka.
18Tsono ngati a mu ufumu wa Satana ayamba kuukirana, Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Paja inu mukuti Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu.
19Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa.
20Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.
21“Munthu wamphamvu akamalonda nyumba yake ali ndi zida zankhondo, katundu wake amakhala pabwino.
22Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa, namgonjetsa, amalanda zida zimene ankazidalirazo, nkugaŵagaŵa katundu amene walandayo.
23 amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.”
45Apo katswiri wina wa Malamulo adati, “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, mukunyozatu ndi ife tomwe.”
46Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe.
47Muli ndi tsoka, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo.
48Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao.
49Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’
50Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi,
51 mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.
52“Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda kiyi yotsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.”
53Pamene Yesu adatuluka m'nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza.
54Cholinga chao chinali chofuna kumtapa m'kamwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.