2 Maf. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Elisa athandiza mkazi wamasiye

1Tsiku lina mkazi wa mmodzi wa m'gulu la aneneri adapita kwa Elisa. Adampempha mokweza kuti, “Mwamuna wanga, amene anali mtumiki wanu, adamwalira. Ndipo inu mukudziŵa kuti mtumiki wanuyo ankaopa Chauta. Tsono kwafika munthu amene mwamuna wanga adakongola zinthu zake, ndipo akuti atenge ana anga aŵiri, kuti akhale akapolo ake chifukwa cha ngongoleyo.”

2Elisa adafunsa maiyo kuti, “Nanga mukuti ineyo nditani? Tanenani, muli ndi chiyani m'nyumba mwanu?” Maiyo adayankha kuti, “Mdzakazi wanune ndilibe nkanthu komwe m'nyumba, koma kambiya ka mafuta basi.”

3Apo Elisayo adamuuza kuti, “Pitani, kabwerekeni mitsuko yambirimbiri kwa anzanu.

4Mukaloŵe m'nyumba mwanu, mukadzitsekere momwemo inuyo ndi ana anuwo. Ndipo mukatsanyulire mafuta m'mbiya zonsezo. Ina ikadzaza, mukaiike pambali.”

5Mai uja adachoka kwa Elisayo, nakadzitsekera ndi ana ake aŵiri aja. Tsono iyeyo ankati akathira mafuta m'mbiya nidzaza, ana ake ankabwera ndi mbiya ina.

6Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja.

7Tsono mai uja adapita kukafotokozera Elisa, munthu wa Mulungu uja. Ndipo Elisayo adauza maiyo kuti, “Mai, pitani mukagulitse mafutawo, ndipo mukabweze ngongole zanuzo. Tsono ndalama zotsala zikhale zothandizira inu ndi ana anu.”

Elisa aukitsa mwana wa mai wina wa ku Sunemu

8Tsiku lina Elisa adapita ku Sunemu kumene kunkakhala mai wina wachuma. Maiyo adaumiriza Elisayo kuti adye chakudya kunyumba kwake. Motero Elisa ankati akamadzera njira imeneyo, nthaŵi zonse ankapatuka kunyumbako nkukadya nao.

9Tsono maiyo adauza mwamuna wake kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti munthu amene amadutsa pano kaŵirikaŵiriyu ngwoyera wa Mulungu.

10Tiyeni timmangire kachipinda kakang'ono kam'mwamba, ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi nyale, kuti nthaŵi zonse akatichezera, azitha kumakakhala m'menemo.”

11Tsiku lina Elisa uja adafika ku Sunemu, nakaloŵa m'kachipinda kam'mwamba kaja kuti akapumule m'menemo.

12Pambuyo pake adauza mtumiki wake Gehazi kuti aitane maiyo. Gehazi adamuitana maiyo, ndipo adafika kwa Elisa.

13Elisa adalamula Gehazi kuti amuuze maiyo kuti, “Ndithu mwavutika potichitira zonsezi. Nanga ife tikuchitireni chiyani? Kodi muli ndi mau oti tikakunenereni kwa mfumu, kapena kwa mtsogoleri wankhondo?” Maiyo adayankha kuti, “Ine ndimakhala mwaufulu pakati pa anthu a mtundu wanga.”

14Ndipo Elisa adafunsanso Gehazi kuti, “Nanga tsono timchitire chiyani?” Gehazi adayankha kuti, “Pepani, mai ameneyu alibe mwana wamwamuna, ndipo mwamuna wake ngwokalamba.”

15Elisa adati, “Tamuitananso.” Ndipo atamuitana, maiyo adaima pa khomo.

16 ai.” Mai uja adati, “Palibe kanthu.”

24Pompo maiyo adaika chishalo nakwera bulu, ndipo adauza wantchitoyo kuti, “Thamangitsa buluyo. Usaleze mpaka ntakuuza.”

25Motero adayenda nakafika kwa Elisa, munthu wa Mulungu uja, ku phiri la Karimele.

Tsono mneneri Elisa ataona kuti mai uja akudza, adauza Gehazi mtumiki wake kuti, “Taona patsidyapo, Msunamu uja akubwera.

26Thamanga msanga ukamchingamire, ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi nkwabwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Nanga mwana uja ali bwino?’ ” Mkaziyo adayankha Gehazi kuti, “Inde, nkwabwino.”

27Tsono atafika kuphiriko kwa Elisa munthu wa Mulungu uja, maiyo adagwada, nagwira mapazi a Elisa. Gehazi adadza kuti amkankhe. Koma Elisa adati, “Mleke, kodi sukuwona kuti ali pa mavuto aakulu? Chauta wandibisira ine zimenezi, sadandiwuze.”

28Tsono mkaziyo adati, “Kodi inu mbuyanga, ine ndidaakupemphani mwana? Kodi suja ndidaakuuzani kuti musandinamize?”

29Elisa adauza Gehazi kuti, “Vala lamba wako, fulumira, utenge ndodo yanga ndipo upite. Ukakumana ndi munthu wina aliyense pa njira, usampatse moni, ndipo wina aliyense akakupatsa moni, usayankhe. Tsono ukagoneke ndodo yangayi pa nkhope ya mwanayo.”

30Apo mai wake wa mwana uja adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine ndiye sindikusiyani ai.” Tsono Elisa adanyamuka natsatira maiyo.

31Gehazi adatsogolako, ndipo adakaigoneka ndodoyo pa nkhope ya mwana uja, koma sipadamveke mau kapena kuwoneka chizindikiro china cha moyo. Choncho Gehaziyo adangobwerera kukakumana ndi Elisa, ndipo adamuuza kuti, “Mwana uja sadauke ai.”

32Elisa ataloŵa m'chipinda muja adaona mwana wakufayo atamgoneka pabedi pake.

33Motero adatseka chitseko nkukhala okha aŵiriwo, ndipo adayamba kupemphera kwa Chauta.

341Maf. 17.21 Tsono adakamgonera mwanayo, nakhudzitsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Ndipo m'mene ankadzitambalitsa choncho pa mwanayo, thupi la mwana uja lidayamba kufunda.

35Elisayo adadzuka nayenda kamodzi cha uku ndi uku m'chipindamo. Kenaka adakamgoneranso mwana uja, ndipo mwanayo adayetsemula kasanunkaŵiri, nkuphenyula maso.

36Pomwepo Elisa adaitana Gehazi nati, “Muitane mai uja.” Iye adamuitana maiyo. Ndipo atabwera, Elisayo adati, “Nayu mwana wanu.”

37Pamenepo maiyo adagwada pa mapazi a Elisa, naŵeramitsa mutu wake pansi. Kenaka adanyamula mwana wake uja, natuluka pa bwalo.

Elisa achita zozizwitsa zina ziŵiri

38Pambuyo pake Elisa adabwereranso ku Giligala, ndipo m'dzikomo munali njala. Tsiku lina Elisa ankaphunzitsa gulu la aneneri, ndipo patapita nthaŵi, adauza mtumiki wake kuti, “Ikapo nkhali yaikulu pa moto, uŵaphikire chakudya a m'gulu la aneneriŵa.”

39Mmodzi mwa aneneriwo adapita ku thengo kukathyola ndiwo. Kumeneko adakapezako mpesa wakuthengo nathyola zipatso zake kudzaza nsalu yake. Adabwera nazo naziduladula, nkuziika m'nkhali muja, osadziŵa kuti nchiyani.

40Tsono adapakula naŵapatsa anthuwo kuti adye. Koma pamene adayamba kudya chakudyacho, anthuwo adafuula kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, muli dziphe m'nkhalimu.” Choncho sadathe kudya chakudyacho.

41Tsono Elisa adaŵauza kuti, “Bwerani ndi ufa.” Elisayo adathira ufawo m'nkhali nati, “Apakulireninso anthu chakudyacho kuti adye.” Ndipo adapeza kuti munalibenso zoopsa m'nkhali muja.

42Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi aŵiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zatirigu zatsopano. Zonsezi adaazitengera m'thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agaŵire anthu chakudyachi kuti adye.”

43Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “Kodi chakudya chimenechi ndingachigaŵe motani kwa anthu 100 onseŵa?” Elisayo adanenanso kuti, “Apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.’ ”

44Motero wantchitoyo adaŵagaŵira anthuwo chakudyacho, naadya, ndipo adasiyako, monga momwe Chauta adaanenera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help