1Mwana wanga, umvetsere bwino zanzeru ndikukuuzazi,
utchere khutu kwa ine womvetsa bwino zinthu,
2kuti uziganiza mochenjera,
ndipo pakamwa pako pazilankhula zanzeru.
3Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi,
mau ake ndi osalala koposa mafuta.
4Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo,
ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5Mapazi ake ndi oloza ku imfa,
poyenda amaloŵera njira yakumanda.
6Njira yamoyo saisamala mpang'ono pomwe.
Njira zake nzokhotakhota,
koma mwiniwakeyo sadziŵako.
7Tsopano, ana inu, mundimvere ine,
musaŵataye mau a pakamwa panga.
8Uzilambalala kutali ndi mkazi wotere,
usamafika kufupi ndi khomo la nyumba yake.
9Mwinamwina ulemu wako udzalanditsa kwa ena,
zaka zako zaunyamata udzazitaya kwa anthu ankhanza.
10Mwinanso alendo adzadyerera chuma chako,
phindu la ntchito zako lidzagwa m'manja
mwa munthu wachilendo.
11Ndipo potsiriza pa moyo wako udzalira chokuwa,
thupi lako lonse litatheratu.
12Pamenepo iwe udzangoti,
“Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo,
mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13Sindidamvere mau a aphunzitsi anga,
sindidatchere khutu kwa alangizi anga.
14Pang'onong'ono, bwenzi nditaonongekeratu
pakati pa mpingo wonse utasonkhana.”
15Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako,
ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako.
16Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse
ngati madzi ongoyenda m'miseu?
17Anawo akhale a iwe wekha,
osatinso uŵagaŵane ndi alendo.
18Uzikhutira ndi mkazi wako,
uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako.
19Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala,
ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale.
Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse,
uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.
20Mwana wanga, ungakopekerenji ndi mkazi wadama,
ungamkumbatire bwanji mkazi wosakhala wako?
21Mayendedwe a munthu Chauta amaŵaona bwino lomwe,
njira zake zonse amazipenyetsetsa.
22Zoipa za munthu woipa zimamtchera msampha iyeyo,
ntchito za machimo ake zimamkwidzinga.
23Amafa chifukwa chosoŵa mwambo,
amatayika chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.