1Ndikulirira Inu Chauta,
ndili m'dzenje lozama lamavuto.
2Ambuye imvani liwu langa.
Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.
3Inu Chauta, mukadaƔerengera machimo,
ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?
4Koma inu mumakhululukira,
nchifukwa chake timakulemekezani.
5Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta,
ndimayembekeza ndi mtima wonse,
ndipo ndimakhulupirira mau ake.
6Mtima wanga umayembekeza Chauta
kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha,
kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.
7Iwe Israele, khulupirira Chauta.
Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika,
ndi wokonzeka kupulumutsa.
8 Mt. 1.21; Tit. 2.14 Adzaombola Israele ku machimo ake onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.