Yes. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo ziŵiri zothokoza

1Tsiku limenelo aliyense mwa inu adzati:

“Ndikukuthokozani Inu Chauta,

pakuti ngakhale mudaandipsera mtima,

mkwiyo wanu udaleka,

ndipo mwandilimbitsa mtima.

2 Eks. 15.2; Mas. 118.14 “Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga,

ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa.

Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa,

ndiye amene ndimamuimbira,

ndiye Mpulumutsi wanga.”

3Mudzakondwera pokatunga madzi

m'zitsime za chipulumutso.

4Tsiku limenelo mudzati:

“Thokozani Chauta,

tamandani dzina lake.

Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

5“Imbirani Chauta nyimbo zotamanda,

pakuti wachita zazikulu.

Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.

6Fuulani ndi kuimba mokondwa,

inu anthu a ku Ziyoni,

pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help