1Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Pitanso, ukakonde mkazi wachigololo amene ali ndi chibwenzi chake. Umkonde monga momwe Ine Chauta ndimakondera Israele, ngakhale iyeyo amapembedza milungu ina, ndipo amakonda kuitsirira nsembe za mphesa zabwino zoumika.”
2Motero ndidamkwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iŵiri ya barele.
3Ndidamuuza mkaziyo kuti, “Uzikhala nane masiku ambiri, osachitanso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina. Nanenso ndidzachita chimodzimodzi.”
4Ndiye kuti Aisraele adzakhala masiku ambiri opanda mafumu kapena akalonga, osapereka nsembe kapena kuimika miyala yachipembedzo, opanda zamaula kapena mafano oombezera.
5Pambuyo pake Aisraelewo adzabwerera ndi kufunafuna Chauta Mulungu wao ndi mdzukulu wa Davide mfumu yao. Nthaŵi imeneyo Aisraele adzagonja kwa Chauta ndipo adzalandira zabwino zake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.