1Tsono Yobe adayankha Chauta kuti,
2“Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse,
chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse.
3 Yob. 38.2 Munandifunsa bwino kuti,
‘Kodi ndiwe yani amene ufuna
kusokoneza uphungu wanga ndi mau opanda nzeru?’
Zoonadi ndidalankhula zimene sindidazidziŵe,
zinthu zodabwitsa kwa ine zimene sindidazimvetse konse.
4 Yob. 38.3 Munandiwuza kuti, ‘Umvetsetse ndipo ndidzalankhula.
Ndidzakufunsa, ndipo iweyo undiyankhe.’
5Ndinkangomva za inu ndi makutu,
koma tsopano ndakuwonani chamaso.
6Nchifukwa chake ndikuchita manyazi
ndi zonse zimene ndidakamba,
ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”
Mulungu adalitsanso Yobe.
7Chauta atalankhula ndi Yobe mau ameneŵa, adauza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira kwambiri pamodzi ndi abwenzi ako aŵiri, chifukwa simudalankhule zabwino za Ine, monga m'mene walankhulira mtumiki wanga Yobe.
8Nchifukwa chake tsopano mutenge ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mupite nazo kwa mtumiki wanga Yobe, mukaperekere nsembe zopsereza. Tsono mtumiki wangayo adzakupemphererani, pakuti pemphero lakelo ndidzalilandira kuti ndisakuchiteni kanthu potsata kupusa kwanu. Inu simudalankhule zabwino za Ine, monga adalankhulira Yobe mtumiki wanga.”
9Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama adapita, nakachita zimene Chauta adaŵauza. Ndipo Chauta adamveradi pemphero la Yobe.
10 Yob. 1.1-3 Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
11Tsono abale ake onse ndi alongo ake omwe, kuphatikizapo onse amene ankamdziŵa kale, adabwera kwa iye nkudzadya naye chakudya m'nyumba mwake. Choncho adampepesa, namuthuzitsa mtima chifukwa cha mavuto onse amene Chauta adaalola kuti amgwere. Tsono aliyense mwa iwowo adampatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12Motero Chauta adadalitsa Yobe pa masiku ake otsirizaŵa kupambana poyamba paja. Tsono adakhala ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ng'ombe 2,000, ndi abulu aakazi 1,000.
13Adabalanso ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu.
14Wamkulu mwa ana aakazi aja adamutcha Yemima. Wachiŵiri anali Keziya, wachitatu anali Kerehapuki.
15M'dziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobe. Bambo wao adaŵapatsa choloŵa chimodzimodzi ngati alongo ao.
16Pambuyo pake Yobe adakhala ndi moyo zaka 140. Tsono adaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mbadwo wachinai.
17Potsiriza Yobe adamwalira, ali nkhalamba ya masiku ochuluka zedi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.