1Pa chaka chachinai cha ufumu wa Dariusi, tsiku lachinai la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa Zekariya uthenga.
2Anthu a ku Betele anali atatuma Sarezere ndi Regemumeleki ndi anthu ao, kuti akapemphe chifundo kwa Chauta.
3Kwinanso adaati akafunse ansembe a ku Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse ndiponso aneneri kuti, “Kodi ifeyo tizilira ndi kusala chakudya pa mwezi wachisanu monga m'mene takhala tikuchitira pa zaka zambiri?”
4Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandipatsa uthenga uwu wakuti:
5“Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo?
6Kodi pamene munkadya ndi kumwa, suja munkangodzikondweretsa nokha?
7Pajatu nzimenezi zija ankanena Chautazi kudzera mwa aneneri akale, pamene munali modzaza ndi anthu ndiponso zinthu zinkapita m'tsogolo mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'mizinda yake yozungulira, ku madera a kumwera ndi ku chigwa.’ ”
Kusamvera kudzetsa ukapolo8Chauta adapatsa Zekariya uthenga uwu wakuti,
9“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Muziweruzana molungama. Muzimverana chisoni ndi kuchitirana chifundo.
10Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu.
11“Koma iwowo adakana kumvera, adandifulatira ndi mtima wokanika. Adatseka makutu ao kuti asamve.
12Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri.
13Poti sadandimvere nditaŵaitana, Inenso sindidaŵamvere atandiitana. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
14Monga momwe amachitira kamvulumvulu, ndidaŵamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu imene iwo sankaidziŵa, ndipo dziko lao lidasanduka chipululu, kotero kuti palibenso wina amene ankayendamo. Choncho dziko lao lokomalo lidasandukadi chipululu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.