Yob. 40 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono Chauta adafunsa Yobe kuti,

2“Kodi munthu wamakaniwe ufuna kukangana ndi Mphambe?

Chabwino, iwe amene unatsutsana ndi Mulungu

uyankhe zimenezo.”

3Apo Yobe adayankha Chauta kuti,

4“Ine sindili kanthu konse!

Kodi ndingathe kukuyankhani chiyani?

Palibe, koma kungogwira pakamwa.

5Ndidalankhula kamodzi, sindiyankhanso.

Ndidalankhula kaŵiri, sindiwonjezanso kanthu kena.”

Mau a Chauta.

6Tsono Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti,

7“Tsopano vala dzilimbe ngati mphongo.

Ndikufunsa mafunso, iweyo undiyankhe.

8Kodi ungandiyese ine wolakwa?

Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?

9Kodi uli ndi mphamvu monga Ine Mulungu?

Kodi mau ako angagunde monga m'mene amagundira mau anga?

10“Ngati zili choncho udzipatse ufumu ndiponso ulemu.

Uvale ulemerero wachifumu.

11Tsanyula mkwiyo wako wosefukira,

uyang'ane aliyense wodzikuza, ndipo umchepetse.

12Uyang'ane aliyense wodzikweza, ndipo umtsitse.

Oipa onse uŵaponderezere pamalo pomwe aliripo.

13Onsewo uŵafwirise pamodzi m'chifwilimbwiti.

Uŵakulunge kumaso m'dziko la anthu akufa.

14Ukatero, nanenso ndidzakuvomereza,

kuti mphamvu zako zakupambanitsadi.

15“Taganiza za mvuu,

Ine ndidaipanga monga momwe ndidapangira iwe.

Imadya udzu ngati ng'ombe.

16Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri,

thupi lake ndi lanyonga zedi.

17Imaimiritsa mchira wake kuti tototo,

ngati mtengo wa mkungudza.

Mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.

18Mafupa ake ndi olimba ngati misiwe yamkuŵa,

nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.

19“Mvuu ndiyo yaikulu mwa zolengedwa za Ine Mulungu.

Ine amene ndidailenga ndidaipatsa maso ake oopsa aja.

20Imapeza chakudya kumtunda

kumene nyama zonse zakuthengo zimaseŵera.

21Imagona patsinde pa zitsamba za mipeta,

imabisalika m'bango ndiponso pa thaŵale.

22Zitsamba za mipeta ndizo zimaipatsa mthunzi.

Misondodzi yamumtsinje imaiphimba.

23Madzi amumtsinje akamakokoma, iyo sichita mantha.

Ngakhale madzi a mu Yordani aiyese m'khosi,

sitekeseka nazo.

24Kodi nanga alipo wina amene

angathe kukola mvuu ndi mbedza

kapena kuikola mu msampha?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help