1“Pa nthaŵi imeneyo Mikaele, mngelo wamkulu amene amalonda anthu akwanu, adzafika. Nthaŵi imeneyo idzakhala ya mavuto oopsa amene sadaonekepo nkale lonse, chilengere cha mtundu woyamba wa anthu mpaka nthaŵi imeneyo. Pa nthaŵiyo anthu ako adzapulumuka, onse amene maina ao adalembedwa m'buku.
2Ambiri mwa amene agona m'nthaka yafumbi adzauka. Ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku manyazi ndi ku chilango chosatha.
3Anthu anzeru adzaŵala kuti ngwee ngati mlengalenga. Ndipo amene adatsogolera anthu ambiri m'njira ya chilungamo adzaŵala ngati nyenyezi mpaka muyaya.
4“Koma iwe Daniele, sunga mauŵa mwachinsinsi, ndipo ulimate bukuli mpaka nthaŵi yomaliza. Ambiri adzathamangira uku ndi uku, ndipo nzeru zidzanka zikulirakulira.”
5Tsono ine Daniele poyang'ana, ndidaona aŵiri ali chilili, wina tsidya lino la mtsinje, wina tsidya ilo.
6Mmodzi adafunsa munthu wovala za bafuta amene anali kumtunda kwa madzi a mtsinjewo kuti, “Kodi zinthu zodabwitsazi zidzatha liti?”
7Munthu wovala bafutayo, amene anali kumtunda kwa madzi, adakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, ndipo ndidamumva akulumbira potchula dzina la Wokhala-moyo-mpaka-muyaya uja kuti, “Zidzakhala zaka zitatu ndi theka. Mazunzo ogwera anthu a Mulungu akadzamalizika, ndi pamene zonsezi zidzathe.”
8Kumva ndidazimva zimenezi, koma sindidazimvetse, ndipo ndidafunsa kuti, “Inu mbuye wanga, nanga zimenezi zidzatha bwanji?”
9Iye adandiyankha kuti, “Pita iwe Daniele, pakuti mau ameneŵa ndi osungidwa mwachinsinsi, ndipo adzakhala obisika mpaka nthaŵi yomaliza itafika.
10Anthu ambiri adzadziyeretsa ndipo adzakhala oyera ndi opanda chodetsa. Koma oipa adzachitabe zoipa. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzamvetse zimenezi, koma amene ali anzeru adzazimvetsa.
11Kuyambira nthaŵi imene nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zidzaletsedwe ndipo Chonyansa chosakaza chija chitakhazikika, padzapita nthaŵi yokwanira ngati masiku 1,290.
12Ndi wodala munthu amene adikira, mpaka kuwona kutha kwa masiku 1,335.
13Koma iwe Daniele ulimbikire njira yako mpaka mathero. Pamenepo udzamwalira, koma udzauka kuti ulandire mphotho pa masiku omaliza.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.