2 Sam. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide agonjetsa Aamoni ndi Asiriya.(1 Mbi. 19.1-19)

1Pambuyo pake Nahasi mfumu ya Aamoni adamwalira, ndipo Hanuni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

2Tsono Davide adati, “Ndidzakhala naye mokhulupirika Hanuni, mwana wa Nahasi, monga momwe bambo wake adaandichitira zabwino.” Motero Davide adatuma atumiki kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika m'dziko la Aamoni.

3Koma akalonga a Aamoni adafunsa Hanuni mbuyawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide wakutumizirani anthu odzakupepesanimu, ndiye kuti akuchitira bambo wanu ulemu? Osati Davide watuma atumiki akewo kwa inu kuti adzafufuze ndi kuzonda mzindawu, ndipo kuti akauwona, auwononge?”

4Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja, naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adaŵadulira zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao.

5Tsono Davide adamva zimenezo, adatuma anthu kuti akaŵachingamire, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye adzabwere kuno.”

6Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, adatuma anthu kukalemba ntchito Asiriya a ku Beterehobu ndi a ku Zoba, ankhondo apansi okwanira 20,000. Adalembanso mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake okwanira 1,000, ndiponso anthu a ku Tobu okwanira 12,000.

7Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu ndi gulu lake lonse la ankhondo, amphamvu okhaokha.

8Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa khomo la chipata cha mzinda. Koma Asiriya a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndiponso anthu a ku Tobu ndi a ku Maaka, anali paokha ku malo opanda mitengo.

9Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele, naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.

10Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni.

11Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iweyo udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ndiye kuti ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza.

12Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”

13Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriya aja kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika.

14Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu.

15Koma Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adasonkanitsa ankhondo ao onse.

16Hadadezere mfumu yao adatuma amithenga kuti akabwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo adafika nawo ku Helamu pamodzi ndi Sobaki, mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.

17Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi.

18Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo Davide adapha anthu apa magaleta okwanira 700, ndi ankhondo okwera pa akavalo okwanira 40,000. Adamvulaza kwambiri Sobaki, mtsogoleri wa gulu lao la ankhondo uja, kotero kuti adafera pomwepo.

19Tsono mafumu onse amene ankatumikira Hadadezere, ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adapangana nawo za mtendere, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya nawonso adaopa kumathandizanso Aamoniwo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help