Mphu. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kulankhula ndi kukhala chete

1Kulipo kudzudzula kwina kochitika pa nthaŵi yosayenera,

ndipo alipo anthu ena achete, koma ali anzeru.

2Kudzudzula nkwabwino kupambana kusunga mkwiyo

mu mtima.

Munthu, wovomera cholakwa, amapulumuka ku chilango.

3Nkwabwino kwambiri kulapa akakudzudzula,

motero udzapewa kuchimwa mwadala.

4Munthu wofuna kukhazikitsa chilungamo mwankhanza,

ali ngati mfule woyesa kuchita dama ndi namwali.

5Mwina munthu amakhala chete,

anthu nkumati ndi wanzeru,

pamene wina amadana naye

chifukwa cha kulongolola kwake.

6Mwina munthu amakhala chete chifukwa chosoŵa choyankha.

Pamene wina amakhala chete chifukwa chodziŵa

nthaŵi yake yolankhula.

7Munthu wanzeru amakhala chete kudikira nthaŵi yoyenera,

pamene wonyada ndi wopusa

sadziŵa kuti nthaŵi yabwino ndi iti.

8Munthu wolongolola anzake samukonda,

munthu woyerekedwa anzake amadana naye.

Mau ozunguza

9Mwina munthu amapeza phindu m'mavuto,

koma mwinanso mwai umasanduka tsoka.

10Mwina mphatso sikupindulira kanthu,

koma mwinanso imakupindulira moŵirikiza.

11Kukonda ulemu kwambiri mwina kumadzetsa manyazi,

komanso mwina anthu otsika amasanduka apamwamba.

12Mwina munthu amagula zinthu zambiri pa mtengo wotsika,

koma nkulipira mobzolera ngati kasanunkaŵiri.

13Munthu wanzeru, anthu amamkonda akamalankhula,

koma kushashalika kwa zitsiru kumangopita padera.

14Mphatso yochokera kwa munthu wopusa sidzakupindulitsa,

chifukwa iye akuyembekeza kulandira ina

yokulapo ngati kasanunkaŵiri.

15Amathandiza pang'ono,

koma amadzudzula kwambiri,

amakuza mau ngati mlaliki.

Lero akongoza mnzake kanthu,

maŵa lino wayamba kulonjelera.

Munthu wotere anzake amadana naye zedi.

16Chitsiru chimati,

“Ine ndilibe bwenzi.

Palibe amene amathokoza ntchito zanga zabwino.

Anthu odya nane ndiwonso amandinyoza.”

17Ndithudi munthu wotere ambiri adzamseka,

ndipo adzamseka kaŵirikaŵiri.

Za kulankhula mosayenera

18Ndi bwino kuterereka pa mwala

kupambana kuterereka pa mau.

Kugwa kwa munthu wochimwa

kumadza choncho modzidzimutsa.

19Munthu wopanda mwambo ali ngati nkhani yosayenera kuikamba,

imene anthu opanda nzeru amaikamba kosalekeza.

20Mwambi wochoka m'kamwa mwa chitsiru anthu amaukana,

popeza kuti chitsirucho chimaunena nthaŵi yosayenera.

21Anthu ena amalephera kuchimwa chifukwa cha umphaŵi,

choncho akamapumula, mtima umakhala uli zii.

22Mwina munthu atha kutaya moyo wake

chifukwa cha manyazi,

mwina atha kuutaya

chifukwa cha maganizo a munthu wopusa.

23Chifukwa cha manyazi wina atha kulonjeza bwenzi lake zinthu,

potero amamsandutsa mdani wake popanda chifukwa.

Za Bodza

24Bodza limaononga mbiri ya munthu,

koma anthu opanda nzeru

bodza silichoka pakamwa pao.

25Mbala ili bwinoko kuposa kamabodza,

komabe aŵiri onsewo chao nchiwonongeko.

26Khalidwe la kunama nloipitsitsa,

munthu wabodza manyazi samuchoka.

Za munthu wanzeru

27Munthu wolankhula zanzeru amakwera yekha,

munthu wa maganizo akucha amakondweretsa akulu.

28Munthu wolima bwino amakolola zambiri,

ndipo munthu wokondweretsa akulu amamkhululukira

zolakwa zake.

29Mphatso ndi zopereka zimadetsa m'maso anthu anzeru,

zimaŵatseka pakamwa, choncho sangathenso kudzudzula.

30Kodi nzeru zobisika ndi chuma chosaoneka zili

ndi phindu lanji?

31Munthu wobisa uchitsiru ali bwinoko

kuposa wobisa nzeru.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help